Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira December 11
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya December 15 ndi Galamukani! ya December. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani zimene munganene kwa munthu amene sakufuna kuti mukambirane, amene wanena kuti, “Sindili wokondwerera.”—Onani buku la Kukambitsirana, tsa. 16.
Mph.15: Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2007. Nkhani ndi kufunsa yoti ikambidwe ndi woyang’anira sukulu. Kambiranani mfundo zofunika kutsindika mumpingo wanu zochokera mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2006. Fotokozani kuti woyang’anira sukulu salengezeratu luso la kulankhula limene wophunzira akugwirirapo ntchito. Popeza m’chaka cha 2007 tidzamaliza kuwerenga Malemba Achiheberi kuyambira Yesaya 24 mpaka kumapeto kwa Malaki, chaka chino chingakhale chabwino kuti abale amene apatsidwa mfundo zazikulu za m’Baibulo ndi ena amene amayankhapo agwiritse ntchito bwino mabuku athu amene amafotokozera mabuku aulosi amenewa. Funsani mafunso ofalitsa awiri kapena atatu. Ofalitsa ake akhale otere: wophunzira watsopano, wophunzira wamng’ono amene akupita patsogolo, ndi wophunzira amene wakhala nthawi yaitali m’sukuluyi. Auzeni kuti anene mmene sukuluyo imawathandizira pa ulaliki wawo ndi pa moyo wawo wauzimu. Limbikitsani onse kuti aziyesetsa kukamba nkhani zomwe apatsidwa, kuyankhapo pa mfundo zazikulu za m’Baibulo, ndi kugwiritsa ntchito mfundo zomwe zimaperekedwa mlungu ndi mlungu kuchokera m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Mph.20: “Musasiye Chikondi Chimene Munali Nacho Poyamba.”a Ngati nthawi ilola, pemphani omvera kuti aperekepo ndemanga pa malemba omwe sanagwidwe mawu.
Nyimbo Na. 193 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 18
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Tchulani za makonzedwe apadera a ulaliki wa kumunda womwe udzachitike pa December 25 ndi pa January 1.
Mph.15: “Bwererani kwa Onse Amene Asonyeza Chidwi Ngakhale Chochepa.”b Pemphani omvera kuti anene zomwe akhala akuchita kuti anthu amene anakumana nawo polalikira mwamwayi kapena pochita ulaliki wa mumsewu awapatse manambala a foni kapena awauze momwe angawapezere. Afotokozenso zokumana nazo zabwino zilizonse zomwe zinakhalapo atachita maulendo obwereza kwa anthu oterowo. Mukhoza kukonzeratu zoti munthu mmodzi kapena awiri adzalankhulepo.
Mph.20: Chikondi ndi Kudzichepetsa ndi Makhalidwe Ofunika Kwambiri mu Utumiki. Nkhani yotengedwa mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2002, masamba 18 mpaka 20, ndime 13 mpaka 20.
Nyimbo Na. 108 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 25
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka. Pogwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 4 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi Galamukani! ya January. Pamapeto pa chitsanzo chilichonse, funsani funso loti aliganizire lomwe lingayankhidwe pa ulendo wotsatira pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.
Mph.15: Zosowa za pampingo.
Mph.20: “Kodi Muli ndi Gawo Lanulanu?”c Muphatikizenso mawu achidule ochokera kwa woyang’anira utumiki onena za malire a gawo la mpingo wanu, zakuti gawo lonse timalifola kangati, ndiponso ngati pali magawo oti munthu angatenge.
Nyimbo Na. 219 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 1
Mph.5: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti a utumiki wa kumunda a December.
Mph.20: Kupereka Lipoti la Mmene Utumiki Ukuyendera. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera kuchokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, kuchokera pa kamutu ka patsamba 83 mpaka kumapeto kwa mutu.
Mph.20: Khalani Ochirimika, Osasunthika. (1 Akor. 15:58) Funsani mafunso ofalitsa kapena apainiya awiri kapena atatu amene atumikira mokhulupirika kwa zaka zambiri. Kodi anaphunzira bwanji choonadi? Kodi ntchito yolalikira inkachitidwa bwanji pamene ankayamba kumene kulalikira? Kodi akumana ndi mavuto otani? Kodi adalitsidwa bwanji chifukwa chochirimika pa kulambira koona?
Nyimbo Na. 65 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.