Ndandanda ya Mlungu wa February 10
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 10
Nyimbo Na. 38 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
jr mutu 7 ndime 7-13 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Genesis 25-28 (Mph. 10)
Na. 1: Genesis 25:19-34 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Anthu Oukitsidwa Kuti Akalamulire ndi Khristu Adzakhala Ngati Iyeyo—rs tsa. 109 ndime 4-8 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Yehova Amaiona Bwanji Nkhani Yopembedza Mafano?—bh tsa. 154-156 ndime 1-5 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 15: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Yohane 4:6-26 ndipo kambiranani mmene mavesiwa angatithandizire mu utumiki. Kambirananinso nkhani yakuti, “Zochitika mu Utumiki Wakumunda” patsamba 4.
Mph. 15: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Lembani Zokhudza Anthu Achidwi.” Nkhani yokambirana. Mukamakambirana kadontho kalikonse komwe kali pansi pa kamutu kakuti, “Kodi Tingachite Bwanji Zimenezi?” pemphani omvera kuti afotokoze chifukwa chake kugwiritsa ntchito mfundo imeneyo, n’kofunika.
Nyimbo Na. 98 ndi Pemphero