Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/01 tsamba 3-6
  • April—Nthaŵi ‘Yogwiritsitsa Ntchito ndi Kuyesetsa’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • April—Nthaŵi ‘Yogwiritsitsa Ntchito ndi Kuyesetsa’
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tingapange Mwezi wa April 2000 Kukhala Mwezi Wathu Wabwino Kuposa Yonse?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • ‘Lalikirani Mokwanira Mawu a Mulungu’
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Chitani Changu pa Zinthu Zabwino!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Khalani “Achangu Pantchito Zokoma” m’April!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 3/01 tsamba 3-6

April—Nthaŵi ‘Yogwiritsitsa Ntchito ndi Kuyesetsa’

1 Kwa anthu a Yehova, milungu yoyandikana ndi Chikumbutso ndi nthaŵi yosinkhasinkha. Ndi nthaŵi yosinkhasinkha zimene imfa ya Kristu inakwaniritsa ndiponso chiyembekezo chimene Mulungu anatipatsa kupyolera m’mwazi wokhetsedwa wa Yesu. Mukaganiza za chaka chatha pa April 19, mumakumbukira chiyani? Kodi mungakumbukire nkhope zimene munaziona usiku wa tsiku limeneli? Mkhalidwe wabwino kwambiri wauzimu umene unali pa Chikumbutso? Nkhani ya Baibulo yofunika kwambiri ndi mapemphero apansi pamtima? Mwina munasankha kusonyeza mokwanira mmene mumayamikirira chikondi chimene Yehova ndi Yesu anakusonyezani. Kodi pakalipano kusinkhasinkha kotereku kukukukhudzani motani?

2 N’zachionekere kuti anthu a Yehova amayamikira osati mwa mawu okha. (Akol. 3:15, 17) Makamaka mu April chaka chatha, tinayesetsa kusonyeza kuyamikira makonzedwe a Yehova a chipulumutso mwa kuchita utumiki wachikristu. Chiŵerengero cha apainiya othandiza chinali 3,076. Khama lawo komanso la anthu ena onse olengeza Ufumu, linathandiza kukhala ndi chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa. Tinasangalala kwambiri kuona kuti anthu anayambitsa maphunziro a Baibulo ochuluka zedi ndiponso kuti tinali ndi chiŵerengero chapamwamba cha opezeka pa Chikumbutso!

3 Ndithudi, kutsimikizika kwa chiyembekezo chathu kumatisonkhezera kugwira ntchito. Zili monga momwe mtumwi Paulo analembera kuti: “Tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira.”—1 Tim. 4:10.

4 Nyengo ya Chikumbutso ino, kodi mudzasonyeza motani kukhulupirira kwanu makonzedwe a Yehova opatsa moyo? Kuyambira mu April chaka chatha takhala ndi ziŵerengero zapamwamba zambiri za ofalitsa. Kodi tingakhale ndi chiŵerengero chapamwamba china mu April akudzayu? Tikhoza kukhala nacho. Koma wofalitsa aliyense, wobatizidwa ndi wosabatizidwa, ayenera kutengamo mbali. Anthu atsopanonso ambiri angayenerere kutengamo mbali. Choncho, pamene mukukonzekera kugwiritsitsa ntchito ndi kuyesetsa mu April akudzayu, lingalirani njira zimene mungalimbikitsire ena, kuphatikizapo atsopano ndiponso osazoloŵera kuti ayende nanu.

5 Kuthandiza Ena Kuyambiranso Kugwira Ntchito: Ngati mukudziŵa ena amene akhala asakuloŵa mu utumiki wakumunda kwa mwezi umodzi kapena iŵiri, mungawalimbikitse ndi kuwapempha kuyenda nanu mu utumiki wakumunda. Ngati ena mu mpingo anazilala, akulu adzayesetsa kuwayendera ndi kuwalimbikitsa kuti mu April ayambirenso.

6 Tonsefe tiyenera kupitiriza kupempha mzimu wa Yehova kuti utilimbitse mu utumiki wake. (Luka 11:13) Kodi tiyenera kuchitanji kuti tilandire mzimu umenewo? Ŵerengani Mawu ouziridwa a Mulungu. (2 Tim. 3:16, 17) Tiyeneranso ‘kumva chimene Mzimu anena kwa Mipingo’ mwa kupezeka pamisonkhano yonse isanu ya mlungu ndi mlungu. (Chiv. 3:6) Ino ndi nthaŵi yabwino kuthandiza anthu ojombajomba ndi ozilala kuwongolera zizoloŵezi zawo za kuphunzira ndi kuyamba kumabwera mokhazikika pamisonkhano. (Sal. 50:23) Tichite zimenezi tikusamaliranso moyo wathu wauzimu. Komabe, m’pofunika chinachake.

7 Mtumwi Petro anafotokoza kuti Mulungu amapatsa mzimu woyera “kwa iwo akumvera iye.” (Mac. 5:32) Kumvera kumeneko kumaphatikizapo kumvera lamulo lakuti “tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni.” (Mac. 1:8; 10:42) Chotero, ngakhale zili zoona kuti polalikira timafunika mzimu wa Mulungu kutilimbitsa, ndi zoonanso kuti tikasonyeza kuti tikufuna kukondweretsa Yehova, umatithandiza kwambiri. Tisapeputse kufunika kwa masitepe oyamba ameneŵa osonyeza kumvera mofunitsitsa!

8 Kuthandiza Ana: Makolo, kodi muli ndi umboni wakuti ana anu akufuna kuuza ena choonadi? Kodi amapita nanu mu utumiki wakumunda? Kodi ndi akhalidwe labwino? Ngati ndi choncho, n’kuchedweranji? Uzani mmodzi wa m’Komiti ya Utumiki ya Mpingo, kuti apende mwana wanuyo ngati akuyenera kukhala wofalitsa mu April akudzayu. (Onani buku la Utumiki Wathu, masamba 99-100.) Dziŵani kuti ana anu angathandize kwambiri kukweza mawu otamanda Yehova mu nyengo ya Chikumbutso ino.—Mat. 21:15, 16.

9 Mayi wina wachikristu ku Georgia, U.S.A, nthaŵi zonse ankalimbikitsa mwana wake wamkazi kuuza ena za Yehova. Chaka chatha, mwanayo ali mu utumiki ndi amayi ake, anagaŵira bulosha la Mulungu Amafunanji kwa bambo wina ndipo anafotokoza mwachidule mitu ya m’katimo. Bamboyo anafunsa kuti: “Uli ndi zaka zingati?” Anati: “Seveni.” Bamboyo anadabwa kuona mwana ngati ameneyo akulalikira mogwira mtima. Mwamunayo anapezeka kuti anakulira m’banja la Mboni koma sanaone choonadi kukhala chofunika kwambiri monga njira ya moyo. Mosakhalitsa, anayamba kuphunzira Baibulo ndi bamboyo, mkazi wake ndiponso mwana wake wamkazi.

10 Ana ambiri ndi ofalitsa, ndipo timasangalala kuyenda nawo mu utumiki. Ana ameneŵa angasonkhezere komanso kulimbikitsa ana anzawo. Komanso April ndi nthaŵi yabwino kwa banja lililonse kulimbitsa unansi wawo ndi kukulitsa uzimu wawo mwa kuyendera limodzi mu utumiki wopatulika. Mitu ya banja iyenera kutsogolera zimenezi.—Miy. 24:27.

11 Kuthandiza Atsopano: Bwanji atsopano amene mukuphunzira nawo Baibulo? Kodi angathandize utumiki mu April akudzayu? N’kutheka kuti pophunzira nawo mutu 2, ndime 22, kapena mutu 11, ndime 14, mu buku la Chidziŵitso anasonyeza kuti akufuna kuuza ena zimene akuphunzira. Ngati muli pafupi kumaliza bukulo, konzekerani kukambirana nkhaniyi momveka pophunzira nawo mutu 18, ndime 8, imene imati: “Mwinamwake mukufunitsitsa kuuza achibale anu, mabwenzi, ndi ena zimene mukuphunzira. Ndipo mwina mwayamba kale kuchita zimenezi mwa njira yocheza, monga momwe Yesu anauzira ena za uthenga wabwino. (Luka 10:38, 39; Yoh. 4:6-15) Tsopano mungafune kuchita zochulukirapo.” Kodi umu ndi mmene zilili ndi amene mukuphunzira nawo?

12 Kodi wophunzira wanu amakhulupirira Mawu a Mulungu? Kodi akugwiritsa ntchito mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo? Kodi wasintha moyo wake kuti ugwirizane ndi miyezo ya Mulungu? Kodi amafika pa misonkhano ya mpingo? Kodi akufuna kutumikira Yehova Mulungu? Bwanji osam’limbikitsa kulankhula ndi akulu kuti aone ngati akuyenera kukhala wofalitsa wosabatizidwa n’kudzayenda nanu mu April? (Onani buku la Utumiki Wathu, masamba 97-9.) Mwanjira imeneyi angaoneretu mmene gulu la Yehova lidzam’chirikizire pamene akuyesetsa kutumikira Yehova.

13 Zoona, ophunzira ena amapita patsogolo mofulumira kuposa ena. N’chifukwa chake, mogwirizana ndi malangizo a mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa June 2000, tsamba 4, ndime 5-6, anthu ambiri akuphunzira buku lachiŵiri ndi anthu amene poyamba anasonyeza chidwi ndipo akufunika thandizo lina kuti agwirizane kwambiri ndi gulu la Mulungu. Timakhulupirira kuti anthu oona mtima ameneŵa adzakhala ophunzira enieni a Kristu, kaya ndi “kukopa pang’ono, kapena ndi kukopa kwambiri.” (Mac. 26:29) Komabe, ngati miyezi imene mwakhala mukuphunzira ndi munthu wotere ikusonyeza kuti ndi wofunika “kukopa kwambiri,” nyengo ya Chikumbutso ino ndi nthaŵi yabwino yoti ayambe kusonyeza kuyamikira dipo la Kristu.

14 Mmene Mungawathandizire Kuyamba Utumiki: Timaphunzira zambiri za mmene tingathandizire oyenerera kuyamba utumiki mwa kupenda mmene Yesu amaphunzitsira ena. Iye samangoti akapeza gulu la anthu n’kuwauza atumwi ake kuti ayambe kulankhula. Amayamba kaye wagogomezera kufunika kwa ntchito yolalikira, kuwalimbikitsa kufunika kwa pemphero, ndiyeno n’kuwapatsa zinthu zitatu zofunika: woyenda naye, gawo, ndi uthenga. (Mat. 9:35-38; 10:5-7; Marko 6:7; Luka 9:2, 6) Mungachitenso zomwezi. Kaya mudzathandiza mwana wanu, wophunzira watsopano, kapena amene wakhala nthaŵi yaitali asakupereka malipoti, n’koyenera kuyesetsa kutsatira izi.

15 Gogomezerani Kufunika Kwake: Muuzeni motsindika kufunika kwa ntchito yolalikira. Sonyezani chimwemwe ponena za ntchitoyi. Simbani zochitika zosonyeza kuti mpingo ukuchita bwino mu utumiki. Sonyezani mzimu umene Yesu anasonyeza wa pa Mateyu 9:36-38. Limbikitsani wofalitsa wam’tsogoloyo kapena wozilala kupempherera kuti aziloŵa nawo mu utumiki komanso kuti ntchito yapadziko lonse iziyenda bwino.

16 M’limbikitseni Kulingalira za Mipata Yambiri Imene Ilipo Yochitira Ulaliki: Muuzeni kuti akhoza kumakasonkhana ndi gulu la phunziro la buku kukakonzekera ulaliki wa kunyumba ndi nyumba. Muuzeni kuti azikambirana ndi achibale ndi anansi kapena kulankhula ndi anzake akuntchito kapena akusukulu pa nthaŵi yopuma. Akakwera zoyendera za anthu onse, angayambe ulaliki mwa kungosonyeza chidwi mwa anthu amene wakwera nawo. Tikayamba ndife, zimatipatsa mpata wochitira ulaliki wogwira mtima. Ndithudi pali mipata yambiri imene tingagwiritse ntchito kuuza ena chiyembekezo chathu “tsiku ndi tsiku.”—Sal. 96:2, 3.

17 Komabe, kungakhale kothandiza kwambiri ngati inuyo mungayambe msanga kuyenda ndi wofalitsa watsopanoyo mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba. Ngati muli ndi cholinga chowonjezera utumiki wanu m’mwezi wa April, funsani mtumiki wa magawo ngati pali gawo lapafupi. Ngati lilipo, zidzakupatsani mpata wofola gawo lonse bwinobwino. Mwachitsanzo, pomaliza kulalikira kapena popita ku misonkhano kapena malo ena, mungaone kuti nyumba imene simunapeze anthu tsopano pali anthu kapena munapezapo anthu achidwi. Ngati n’koyenera, dzawachezereni mwachidule nthaŵi imene idzakhale yabwino kwambiri. Kuteroko, kudzakuthandizani kukhala wokhutira komanso wachimwemwe mu utumiki.

18 Konzekerani Uthenga Wosangalatsa: Kufuna kulalikira uthenga wa Ufumu n’kosiyana ndi kutsimikizira zimene mukunena, makamaka akakhala watsopano kapena wakhala nthaŵi yaitali asakupita mu utumiki. Kuthandiza atsopano ndi ozilala kukonzekera n’kopindulitsa. Utumiki wakumunda ndiponso misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda zimapereka malingaliro othandiza, koma sizitanthauza kuti musakonzekere panokha.

19 Kodi mungathandize motani atsopano kukonzekera utumiki? Yambani ndi ulaliki wa magazini, konzani ulaliki wosavuta ndiponso wachidule! Afunseni nkhani za pa nyuzi zimene zingachititse chidwi anthu a m’gawolo, ndiyeno pezani mfundo m’magazini yatsopano imene ikugwirizana ndi zimenezo. Yesererani ulalikiwo pamodzi, ndipo ngati n’kotheka ugwiritseni ntchito mu utumiki mosataya nthaŵi.

20 Thandizani Kuti M’tsogolo Tidzachuluke: Chaka chatha opezeka pa Chikumbutso anali oposa 14.8 miliyoni. Amene anapereka malipoti monga ofalitsa anali oposa pang’ono 6 miliyoni. Kutanthauza kuti pafupifupi anthu 8.8 miliyoni anali ongosangalatsidwa kufika pa pulogalamu yapadera imeneyi kumene anamvetsera nkhani imene imafotokoza chimodzi mwa ziphunzitso zikuluzikulu za Baibulo. Ena anadziŵana nafe, zimene mosakayikira zinawasangalatsa. Ambiri amatiyamikira kwambiri, kuchirikiza ntchito yathu yapadziko lonse ndiponso kutiikira kumbuyo pamaso pa ena. Anthu onseŵa ndi oti akhoza kudzachulukitsa chiŵerengero m’tsogolo. Kodi tingawathandize motani kuti apitirize kupita patsogolo?

21 Ambiri amene amafika pa Chikumbutso ndi oyitanidwa ndi wina wa ife. Kutanthauza kuti nthaŵi zambiri, pagululo pamakhala amene akumudziŵa. Ngati wina wabwera chifukwa chakuti tinamuitana, tili ndi udindo womulandira bwino ndi kumuthandiza kupindula kwambiri ndi pulogalamuyo. Popeza holo idzakhala yodzaza, m’thandizeni kupeza malo okhala. M’bwerekeni Baibulo, ndipo onerani limodzi nyimbo yanu. Yankhani mafunso onse amene angafunse. Kumusamala ndi kumusonyeza kwanu chikondi kungathandize kwambiri kukulitsa chidwi chimene ali nacho. Komabe, umenewu ndi udindo wa tonse—ngati taona munthu wachilendo, m’landireni ndi manja aŵiri ndipo lankhula nayeni mwachidule kuti mudziŵane naye.

22 Kufika pa Chikumbutso kungakhudze kwambiri maganizo a munthu. Kufika pa msonkhano kokhako kungasonyeze kuti kulibe kumene wapeza zimene akufufuzazo ndiponso kuti tili ndi zina zimene akufuna kupenda mosamala. Kwa munthu amene sadziŵa kuti chikondi cha Yehova chilibe malire, kumuuza za makonzedwe apadera a dipo kungam’tsegule maso zedi. Angaone mosavuta kuti ndife osiyana, oona mtima, aubwenzi, achikondi, ndi aulemu. Holo yathu siifanana n’komwe ndi zimene amaona m’matchalitchi amene amaonetsa mafano ndi miyambo yopanda tanthauzo. Mwachidziŵikire atsopano adzaona kuti anthu opezekapo ndi osiyanasiyana ndiponso kuti sayendetsa mbale ya zopereka. Zinthu zimenezi zingawasonkhezere kwambiri kudzabweranso.

23 Pambuyo pa Chikumbutso, wina ayenera kukhala tcheru kuthandiza watsopano aliyense amene anafika pachikumbutso. Ngati munaitana atsopano, muli ndi udindo wapadera. Asanapite, onetsetsani kuti mwawauza misonkhano ina imene imachitika pa Nyumba ya Ufumu. Tchulani mutu wa nkhani yapoyera ya mlungu ukudzawo. Adziŵitseni malo ndi nthaŵi ya Phunziro la Buku la Mpingo lapafupi ndi kwawo. Ndiyeno, dzaŵapatseni buku la Banja, ndipo apempheni kuti apite nanu ku phunziro la buku. Fotokozani chifukwa chake mpingo wonse ukukonzekera kupita ku msonkhano wachigawo wapafupi ndi kwawoko umene uchitike posachedwapa.

24 Konzani zokawachezera kunyumba kwawo. Onetsetsani kuti ali ndi bulosha la Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso, limene lidzawaphunzitsa ziphunzitso zazikulu za m’Baibulo. Ngati sanayambe kuphunzira, apempheni kuti muziphunzira nawo Baibulo. Auzeni kuti aŵerenge bulosha la Mboni za Yehova, limene limapereka chithunzi chabwino kwambiri cha mmene ntchito yathu imayendera monga gulu. Konzani kuti aonane ndi ena mu mpingo. M’miyezi ikubwerayi, pitirizani kuchezera anthu achidwi; apempheni kufika pamisonkhano mukakhala ndi woyang’anira dera kapena msonkhano wadera kapena tsiku la msonkhano wapadera. Apatseni mwayi uliwonse wosonyeza kuti ndi “ofuna moyo wosatha”!—Mac. 13:48, NW.

25 Zimene Akulu Angachite: Kuti utumiki uyende bwino mu April akubwerayu zidzadalira kwambiri akulu. Ngati mumachititsa phunziro la buku, lembani zimene mungachite pothandiza a m’gulu lanu onse kutenga mbali mu ntchito yapaderayi. Kodi m’gulu lanulo muli ana, atsopano, ojombajomba, kapena ozilala? Onani ngati makolo, apainiya, kapena ofalitsa ena akuthandiza anthu ameneŵa. Athandizeni mwa njira iliyonse imene mungakwanitse. Mlongo wina amene anali wojombajomba mu utumiki wakumunda kwa zaka ziŵiri anathera maola oposa 50 mu utumiki m’mwezi wa April chaka chatha. N’chiyani chinam’pangitsa kusintha? Akuti ndiwo ulendo waubusa wolimbikitsa umene akulu anachita.

26 Akulu ndi atumiki otumikira ayenera kugwirizana kuti atsimikizire kuti pali gawo lokwanira, magazini okwanira, ndi mabuku okwanira mwezi ukudzawu. Kodi angawonjezere misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda? Ngati ndi choncho, dziŵitsani anthu za makonzedwe apaderaŵa. Koposa zonse, m’mapemphero anu a pamaso pa anthu ena ndi a m’seri, m’pempheni Yehova kudalitsa mwezi wathu wa ntchito ya Ufumu yochuluka.—Aroma 15:30, 31; 2 Ates. 3:1.

27 Chaka chatha mu April, mpingo wina ku North Carolina, akulu analimbikitsa kwambiri kuchita zochuluka mu utumiki. Mlungu uliwonse pamisonkhano, anali kupempha ofalitsa kupenda mwapemphero ngati angalembetse upainiya wothandiza. Nthaŵi iliyonse, akulu ndi atumiki otumikira onse analimbikira kunena kuti April ukhale mwezi wabwino kwambiri kuposa ina yonse. Choncho, 58 peresenti ya ofalitsa, komanso akulu ndi atumiki otumikira onse anachita upainiya mwezi umenewo!

28 Mapindu Ogwira Nawo Ntchito Mokwanira: Kodi timapindulanji mwa ‘kugwiritsitsa ntchito ndi kuyesetsa’ mu utumiki? (1 Tim. 4:10) Ponena za kugwira kwawo ntchito mwachangu pa mpingo mu April chaka chatha, akulu atchulidwa pamwambaŵa analemba kuti: “Nthaŵi zambiri abale ndi alongo amakamba za chikondi ndi unansi umene ali nawo pakati pawo chiyambireni kuchita zochuluka mu utumiki wakumunda.”

29 Mbale wina wachinyamata amene amayenda movutikira ankafunitsitsa kuchita nawo ntchito yapaderayi mu April chaka chatha. Mwa kukonzekera bwino ndiponso mothandizidwa ndi amayi ake ndiponso abale ndi alongo ake auzimu, anasangalala ndi mwezi wabwinowu monga mpainiya wothandiza. Kodi anamva bwanji ndi zimene anachita? Anati: “Kwa nthaŵi yoyamba, ndinaona ngati thupi langa ndi labwinobwino.”

30 Sizokayikitsanso kuti Yehova amadalitsa kwambiri amene amalemekeza kwambiri mwayi wawo wolankhula ndi ena za Ufumu wake. (Sal. 145:11, 12) Pamene tikukumbukira imfa ya ambuye, timadziŵa kuti madalitso akudzipereka kwa umulungu adzakhala ochuluka zedi m’tsogolo. Mtumwi Paulo analakalaka mphoto ya moyo wosatha. Komabe, anadziŵa kuti sinali nkhani yokhala duu n’kumayembekezera zinthu kuchitika. Analemba kuti: “Kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.” (Akol. 1:29) Yehova kupyolera mwa Yesu, anam’patsa mphamvu Paulo kuti akwaniritse ntchito yopulumutsa moyo, ndipo angatichitire zofananazo lerolino. Kodi zimenezi n’zimene zidzakuchitikireni April akubwerayu?

[Bokosi patsamba 3]

Kodi Inuyo Mudzalimbikitsa Ndani Kukhala Wofalitsa mu April?

Mwana wanu?

Wophunzira Baibulo?

Munthu amene wazilala?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena