Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/96 tsamba 3-4
  • Khalani “Achangu Pantchito Zokoma” m’April!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani “Achangu Pantchito Zokoma” m’April!
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Lalikirani Mokwanira Mawu a Mulungu’
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Kodi Tingapange Mwezi wa April 2000 Kukhala Mwezi Wathu Wabwino Kuposa Yonse?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • “Akuchuluka m’Ntchito ya Ambuye”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • April—Nthaŵi ‘Yogwiritsitsa Ntchito ndi Kuyesetsa’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 4/96 tsamba 3-4

Khalani “Achangu Pantchito Zokoma” m’April!

1 M’ngululu yapitayo umboni waukulu koposa unachitidwa pamene mamiliyoni a makope a Uthenga wa Ufumu No. 34 anagaŵiridwa padziko lonse. Onse pamodzi ofalitsa ndi apainiya m’mipingo anatengamo mbali mwachangu m’ntchito yosangalatsa imeneyi. Kodi munali mmodzi wa iwo? Ngati zili choncho, mosakayikira munasangalala kwambiri kukhala ndi phande m’mkupiti wabwino kwambiri umenewo. Tsopano mungamafunse kuti, Kodi ndi ‘ntchito yokoma’ yotani imene ikutiyembekezera chaka chino?—Tito 2:14.

2 M’April ndi kuchiyambi kwa May, tidzasangalala kugaŵira kope lapadera la magazini a Galamukani!, kope la May 8, 1996, lokhala ndi nkhani yakuti “Pamene Sikudzakhalanso Nkhondo.” Popeza kuti nkhani imeneyi idzakopadi eni nyumba ambiri, tidzayenera kugaŵira magazini ameneŵa pamlingo waukulu koposa. Chifukwa cha kufunika kwa uthenga umene lili nawo, kope limeneli la Galamukani! liyenera kugaŵiridwa m’April mpaka m’May, kufikira mitokoma yonse itatha.

3 Chonulirapo Chathu—Kutengamo Mbali kwa Ofalitsa Onse: Kungakhaledi kolimbikitsa ngati wofalitsa aliyense m’dziko lino adzatengamo mbali m’ntchito yolalikira m’April. Pomakumbukira bwino lomwe Chikumbutso cha imfa ya Kristu, tidzayenera kusonyeza chiyamiko chathu kaamba ka ubwino wa Mulungu mwa kupereka “nsembe yakuyamika” mwachindunji mu utumiki wakumunda.—Aheb. 13:15.

4 Kuyesetsa kwakhama nkofunika kuti mudziŵe zosoŵa za wamumpingo aliyense kotero kuti onse akakhalemo ndi phande mwachangu mu utumiki m’April. (Aroma 15:1) Ochititsa phunziro la buku ayenera kudziŵa bwino lomwe za mkhalidwe wa awo omwe ali m’magulu awo ndi kupereka chithandizo chogwira ntchito ngati nchofunika. Kodi pali amene akufuna choyendera ulendo? Kodi ndani angachipereke? Kodi ena ngamantha kapena ngamanyazi? Kodi ofalitsa achidziŵitso kwambiri angagwire nawo ntchito? Bwanji ponena za obindikiritsidwa m’nyumba kapena odwala? Kodi angachite ulaliki wapatelefoni, wa m’makalata, kapena njira ina yogwira ntchito?

5 Ena amene anafooka akhala akulandira chilimbikitso chauzimu nthaŵi zonse, ndipo angafunitsitse kuloŵanso m’ntchito ya kulalikira. Mkupiti umenewu wa Galamukani! wapadera udzawapatsa mwaŵi wapadera kwambiri wakuti akhalenso achangu.

6 Phunzitsani Achichepere Kutengamo Mbali: Ana ambiri a Mboni za Yehova atsagana ndi makolo awo kunyumba ndi nyumba kwa zaka zingapo, ngakhale kuti sanayambebe kutumikira monga ofalitsa osabatizidwa. Kodi inoyo ndiyo nthaŵi yakuti ayambe? Kodi ali osonkhezeredwa kuchokera pansi pamtima ndi okonzekera kukhalamo ndi phande kwatanthauzo m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba? Mitu ya mabanja iyenera kugwiritsira ntchito nthaŵi ya pa phunziro la Baibulo la banja kuthandizira ana awo oyeneretsedwa kukonzekera ulaliki woyenerera misinkhu yawo ndi kukhoza kwawo. Osinkhukirapo angasankhe funso lotokosa maganizo limene adzagwiritsira ntchito kudzutsa chidwi cha mwini nyumba ndiyeno kusonyeza yankho lake m’magaziniwo. Ana ocheperapo msinkhu angapereke ulaliki wogwira mtima m’mawu ochepa chabe. Mwachitsanzo, angalimbikitse mwini nyumba kuti “aŵerenge magazini apadera amene akugaŵiridwa padziko lonse mwezi uno.” Monga mbali ya kukonzekera kwa banja lanu, tsimikizirani kutchulapo njira zochitira ndi zopinga zofala. Mudzapeza malingaliro abwino angapo m’buku la Kukambitsirana. Panthaŵi yachakudya ndi panthaŵi zina zoyenera, limbikitsani a m’banja kusimba zimene apeza mu utumiki wakumunda.

7 Ophunzira Baibulo Oyeneretsedwa Amachita Ntchito Imene Yesu Anachita: Kaphunzitsidwe ka Yesu sikanali kokha pa malangizo a nkhani za ziphunzitso. Anatsagana ndi ophunzira ake mu utumiki nawaphunzitsa kulalikira. (Luka 8:1; 10:1-11) Kodi mkhalidwe ngwotani lerolino? Maphunziro a Baibulo oposa 27,000 akuchititsidwa m’Malaŵi. Mosakayikira, atapeza chilimbikitso choyenera ambiri a ophunzirawa angatenge sitepe lotsatira m’kuphunzira kwawo ndi kuyeneretsedwa kutumikira monga ofalitsa osabatizidwa m’April.

8 Ngati mumachititsa phunziro la Baibulo, talingalirani mafunsowa: Kodi wophunzirayo akupita patsogolo, malinga ndi msinkhu wake ndi kukhoza kwake? Kodi wayamba kuuza ena za chikhulupiriro chake atapeza mpata? Kodi iye wavala “umunthu watsopano”? (Akol. 3:10, NW) Kodi ali ndi ziyeneretso za ofalitsa osabatizidwa, zofotokozedwa pamasamba 97 mpaka 99 m’buku la Uminisitala Wathu? Ngati muli otsimikizira kuti ngwoyenerera, bwanji osakambitsirana naye nkhaniyo? Ophunzira ena amangofuna kuitanidwa mwachindunji kuti agaŵanemo m’ntchitoyi. Komabe, ngati wophunzirayo ngwofunitsitsa, woyang’anira wotsogoza choyamba adzafunikira kulinganiza kuti akulu aŵiri akambitsirane nanu monga mwa nthaŵi zonse. Nthaŵi zina, chinachake chingamaletse wophunzira. Mwinamwake mmodzi wa akulu angatsagane nanu ku phunziro la Baibulo ndi kusonkhezera wophunzirayo kufotokoza malingaliro ake ponena za choonadi. Atamvetsera zimene wophunzirayo anganene, mkuluyo angathe kupereka njira zogwira ntchito, pamodzi ndi thandizo lochokera m’Malemba.

9 ‘Chitani Machawi’ Kuti Muchite Upainiya Wothandiza: Chaka chilichonse panthaŵi ya Chikumbutso, kuyamikira dipo kumasonkhezera zikwi ‘kuchita machawi’ kuti akhale apainiya othandiza. (Aef. 5:15-17) Ngakhale kuti pamafunika kudzimana, mfupo zake nzazikulu. Chiŵerengero chabwino cha achichepere amagwiritsira ntchito tchuthi chakusukulu kuti achite upainiya wothandiza. Achikulire amene amagwira ntchito yolembedwa amagwiritsira ntchito bwino madzulo ndi kutha kwa milungu m’ntchito imodzimodziyo. Motero, mabanja athunthu achita upainiya wothandiza pamodzi! M’mipingo ina ambiri a akulu ndi atumiki otumikira ndi akazi awo alembetsa upainiya wothandiza. Posonkhezeredwa ndi chitsanzo chawo chachangu, ena atsatira zimenezo, kotero kuti peresenti yaikulu ya mpingo amatumikira monga apainiya othandiza m’April.

10 Kaya mudzakwanitsa kuchita upainiya wothandiza kapena ayi, funani njira zowonjezerera utumiki wanu wakumunda m’April. Dziikireni chonulirapo chaumwini, chimene chidzafuna kuyesetsa kuti muchifitse koma chofikika. Chikhumbo chanu cha ‘kupereka ndi kuperekedwa konse’ mu utumiki wa Yehova, malinga ndi mikhalidwe yanu, chidzakhala ndi dalitso lake.—2 Akor. 12:15.

11 Misonkhano Yokonzekera Utumiki Wakumunda: Misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda iyenera kulinganizidwa tsiku lililonse la mkupiti wa Galamukani!, panthaŵi imene idzalola utumiki kuyamba msanga. Makonzedwe ayenera kupangidwanso kaamba ka ulaliki wa mmadzulo. Ofalitsa ambiri adzakhala akuchita utumiki wakumunda pakutha kwa milungu, motero mipingo iyenera kukonza misonkhano yokonzekera utumiki pamasiku a Loŵeruka, mmaŵa ndi masana omwe, kwanthaŵi yonse ya kugaŵira Galamukani! kwapadera.

12 Awo amene amachititsa misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda ayenera kutsimikizira kuti pali gawo lokwanira. Gawo limene silinagwiridwemo ntchito papitapa liyenera kufoledwa choyamba. Kodi muli ndi ndime imodzi kapena zingapo zimene sizinafoledwe papitapa? Ngati mudzafuna thandizo kuzifola mkati mwa mkupitiwu, lankhulani ndi woyang’anira utumiki kapena ndi mbale wosamalira gawo ndipo adzakhala ofunitsitsa kupanga makonzedwe akuti muthandizidwe.

13 Kodi Mudzagaŵira Magazini Angati? Aliyense payekha ayenera kuyankha funso limenelo. Pofuna kudziŵa chiŵerengero cha magazini amene mungagaŵire mkati mwa mkupiti, lingalirani za mtundu wa ndime imene mudzagwiramo ntchito, msinkhu wanu, thanzi lanu, nthaŵi imene mungagwiritsire ntchito, ndi mbali zina. Komabe, musaiŵale chikumbutso chimene chinaperekedwa m’kope la January 1, 1994 la Nsanja ya Olonda chakuti: “Monga mwa lingaliro, ofalitsa akhoza kukhala ndi chonulirapo, tinene kuti, magazini 10 pamwezi, zikumadalira pa mikhalidwe yawo; apainiya akhoza kumenyera chiŵerengero cha 90.” Kodi chonulirapo chofananacho chingakhale chofikirika kwa inu?

14 Akulu—Kulinganiza Kwabwino Nkofunika: Tsimikizirani kuti gawo lonse la mpingo lidzafoledwa ndi kope lapadera la Galamukani!, ngati nkotheka. Payenera kukhala chisamaliro chapadera pogwira ntchito mu gawo lamalonda lililonse la mpingo. Awo amene adzalifola ayenera kukhala okonzekera bwino ndi ovala bwino. Ulaliki wautali siwofunikira. Polankhula ndi wamalonda, munganene kuti nthaŵi zambiri anthu amalonda simumawapeza panyumba, motero mukumuchezera pamalo ake amalonda kumusonyeza nkhani imene idzamukondweretsa mosakayikira. Ndiyeno mwachidule mungafotokoze nsonga yakutiyakuti m’magaziniwo. Ulaliki wam’khwalala ndi magazini m’gawo lampingo uyenera kukhalanso wolinganizidwa bwino. Njira yabwino kwambiri pochita ulaliki wam’khwalala ndiyo kuyamba kufikira anthu odutsa, m’malo mowayembekezera kuti adze kwa inu. Popeza mudzakhala mukuonedwa ndi anthu ambiri, muyenera kusamala kukhala ndi maonekedwe aulemu. Pangakhale malo ena m’gawo lanu amene mungagwiriremo ntchito mkati mwa mkupiti, monga mabwalo a ndege, zipatala, poimika galimoto, ndi nyumba zosungiramo okalamba ndi odwala. Bungwe la akulu liyenera kudziŵa makonzedwe oyenera amene angapangidwe kaamba ka kulalikira m’malo a gawo la mpingo wanu ameneŵa.

15 Yehova ali wantchito wosatopa. (Yohane 5:17) Analenga kumwamba ndi dziko lapansi limodzinso ndi zomera ndi nyama; koma anapitirizabe kugwira ntchito mpaka atalenga munthu—ntchito yake yodzetsa ulemerero padziko lapansi. Kukhala kwathu ndi moyo kuli chotulukapo chachindunji cha kufunitsitsa kwa Mulungu kugwira ntchito. Monga “akutsanza a Mulungu,” tiyenera kusonkhezeredwa ndi chikondi chathu pa iye kukhala “achangu pantchito zokoma.” (Aef. 5:1; Tito 2:14) Popeza Yehova ngwoyenerera kulandira ntchito zathu zabwino koposa ndipo popeza munthu wachangu amakhala ndi chikhumbo cha kupeza zotulukapo, tiyenera kufunitsitsa kuchita ntchito yabwino koposa mu utumiki. Zoonadi, Yehova amayamikira nsembe iliyonse imene tipereka kwa iye, ndipo ntchito yathu siili konse yachabe. (1 Akor. 15:58) Motero, ndi mitima yachiyamiko, tiyeni tigwire ntchito mwachangu m’April, ndi chidaliro chakuti Yehova adzatiyanja ndi kutidalitsa ndi kuti tidzapeza chipambano chachikulu!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena