Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/95 tsamba 3-4
  • “Akuchuluka m’Ntchito ya Ambuye”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Akuchuluka m’Ntchito ya Ambuye”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Gaŵirani Uthenga wa Ufumu Na. 35 Kulikonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • “Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu ndi Lotani?”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Tidzakhala ndi Ntchito Yapadera Kuyambira pa October 16 Mpaka pa November 12
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Khalani “Achangu Pantchito Zokoma” m’April!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 4/95 tsamba 3-4

“Akuchuluka m’Ntchito ya Ambuye”

1 Mosakayikira, tidzakhala otanganitsidwa m’ntchito zateokrase m’April ndi May! Pa April 14 tidzakhala ndi phwando la Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Anthu ambiri ayenera kulimbikitsidwa kudzapezekapo pa chochitika chofunika kwambiri chimenechi: ochita nawo malonda, achibale osakhulupirira, anzathu akusukulu, okondwerera achatsopano, ndi ophunzira Baibulo. Pangani ndandanda ya amene mudzafuna kuwaitanira kotero kuti musaphonyepo aliyense.

2 Mlungu wotsatira Chikumbutso tidzalimbikitsa onse amene adzapezekapo kudzamvetsera nkhani yapoyera yapadera pa April 23, ya mutu wakuti “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ali Pafupi.” Tikhulupirira kuti okondwerera ambiri amene adzamva uthenga wosabisa kanthu umenewu adzaona kufunika kwa kuyanjana ndi mpingo mokhazikika, osati pa zochitika zapadera zokha.

3 Uthenga wa Ufumu Wapadera Udzatulutsidwa: Mbali yapadera ya msonkhano wa pa April 23 idzakhala kutulutsidwa kwa Uthenga wa Ufumu Na. 34 wapanthaŵi yake wamasamba anayi umene udzagaŵiridwa kwambiri kufikira pa May 14. Kodi simukuvomereza kuti tidzakhala “akuchuluka m’ntchito ya Ambuye” mkati mwa nyengo ya Chikumbutso imeneyi?—1 Akor. 15:58.

4 Mpingo uliwonse udzagaŵiridwa mtokoma wake wa Uthenga wa Ufumu. Mabokosi okhalamo Uthenga wa Ufumu ayenera kusungidwa m’malo osungika ndipo sayenera kuwatsegula kufikira mapeto a programuyo pa April 23. Panthaŵiyo Uthenga wa Ufumu udzagaŵiridwa kwa abale ndi anthu ena. Pamapeto a misonkhano ya mpingo, misonkhano yadera, kapena maprogramu a tsiku la msonkhano wapadera pa April 23, aja opezekapo adzalandira mmodzi ndi mmodzi kope lake kotero kuti adziŵe za mkati zake ndi kukhala okonzekera kuligaŵira.

5 Akulu Adzakhala ndi Zambiri Zochita: Kuchiyambi kwa mwezi umenewu, bungwe la akulu liyenera kukumana ndi kukambitsirana zofunika za mkupiti wapadera umenewu. Mipingo iyenera kuyesayesa kufola gawo lawo lonse. Mkupitiwo usanathe, pangani kuyesayesa kwapadera kwa kugwira ntchito m’ndime zimene sizinafoledwe kwa miyezi isanu ndi umodzi yapitayo. Poona kufunika kwa ntchitoyo, tidzafuna kupatula nthaŵi yaikulu ya utumiki. Mosakayikira, ofalitsa ochuluka kwambiri adzalembetsa upainiya wothandiza. Mwachionekere, ophunzira Baibulo ambiri adzagwirizana nafe mwa kukhala ofalitsa osabatizidwa ovomerezedwa chatsopano. Ha, tidzakhala ndi nthaŵi yosangalatsa chotani nanga yogwirira pamodzi ntchito ya Ambuye!

6 Ochititsa Phunziro Labuku Lampingo ayenera kupanga makonzedwe otsimikizirika a umboni wa kagulu pamasiku a Loŵeruka ndi Sande. Aliyense ayenera kulimbikitsidwa kukhala ndi phande mokangalika. Kuwonjezera pa ntchito ya kumapeto kwa mlungu, umboni wa madzulo uyenera kulinganizidwa mosachepera pa kamodzi pa mlungu mkati mwa mkupitiwo. Ena angakonde kukumana kaamba ka utumiki wakumunda pambuyo pa sukulu kuti apatse mwaŵi ana a sukulu amene angafune kukhala ndi phande lowonjezereka.

7 Kukumana kwa utumiki wakumunda kuyenera kulinganizidwa mwa njira yakuti ofalitsa ndi apainiya aloŵe mwamsanga mu utumiki tsiku lililonse. Kukumana kumeneku kuyenera kukhala kwachidule. Kulikonse kuyenera kukhala ndi chitsanzo chachidule cha kugaŵira Uthenga wa Ufumu. Kukumana kwa masana kwa utumiki wakumunda kungaphatikizepo lingaliro limodzi kapena aŵiri onena za maulendo obwereza kwa aja amene alandira Uthenga wa Ufumu. Komabe, ofalitsa ena angakonde kuugaŵira mmaŵa ndi masana omwe. Chifukwa chake, woyang’anira utumiki ayenera kutsimikizira kuti ndime zokwanira zilipo. Dzina ndi keyala ya aliyense amene asonyeza chikondwerero ziyenera kulembedwa pa cholembapo za kunyumba ndi nyumba. Mfundo zazikulu za kukambitsirana kwachidule zingalembedwe m’danga la mawu. Zimenezi zidzatsegulira njira ulendo wobwereza patsiku lina la mlunguwo kapena mweziwo.

8 Ngati mpingo wina uthandiza wina kufola gawo lake, maina ndi makeyala a anthu okondwerera ayenera kuperekedwa ku mpingo wa gawolo.

9 Makolo, kodi ana anu akupita patsogolo kulinga ku kukhala ofalitsa osabatizidwa? Kwaonedwa kuti m’mipingo ina, ana odzisunga atsagana ndi makolo awo odzipatulira mu utumiki kwa zaka zingapo, ndipo anawo akuchita bwino, ngakhale kuti sanakhalebe ofalitsa a uthenga wabwino. Makolo ayenera kuona ngati kuti ana awo akuyenereradi mwaŵi umenewu. Akulu aŵiri angakambitsirane mfundo zonse ndi mutu wa banja ndi kuona ngati kuti mwanayo angaŵerengeredwe monga wofalitsa wosabatizidwa.—om tsa. 99-100.

10 Kodi pali ofalitsa alionse m’gawo la mpingo wanu amene salinso okangalika pakupereka nsembe ya chitamando kwa Yehova? (Aheb. 13:15) Ofooka ena angakhale atagonjetsedwa mwa kulefulidwa kapena ndi nkhaŵa za moyo, ngakhale kuti akupitiriza kutsatira miyezo ya Baibulo ya makhalidwe. Kuchezeredwa mwaubwenzi ndi mmodzi wa akulu kungawasonkhezere kuyambanso kuyanjana mokhazikika ndi mpingo, ndipo panthaŵi yoyenera, angayambenso ntchito ya utumiki.

11 Onse Oyeneretsedwa Angakhale ndi Phande m’Ntchito Yosangalatsa Imeneyi: Kodi ena a inu ana, ndi inu anyamata ndi asungwana kumakuvutani kukhala ndi phande mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba? Bwanji ponena za inu atsopano amene simunazoloŵere kwambiri ntchito yolalikira? Mudzapeza kuti kugwira ntchito ndi Uthenga wa Ufumu wapadera umenewu kuli kosangalatsa kwambiri! Chimene chimangofunika ndicho ulaliki wosavuta.

Munganene zonga izi:

◼ “Mwezi uno tikugaŵira uthenga wofunika kwambiri m’maiko 232 padziko lonse. Uthengawo uli wofunika chifukwa chakuti umatipatsa zifukwa zamphamvu zokhulupirira kuti pali njira yothetsera mavuto amene tikukumana nawo lerolino. Tikufuna kuti mukhale ndi kope lanulanu.”

Kapena mungayese izi:

◼ “Mwezi uno anthu odzipereka pafupifupi 5 miliyoni akugaŵira uthenga wofunika m’zinenero zambiri. Uthengawo walembedwera anthu amene afuna kuona kutha kwa mavuto amene tonsefe tikukumana nawo lerolino. Ili ndi kope lanu.”

Ulaliki wosavuta uwu ungakuyenereni:

◼ “Tikulimbikitsa aliyense kuŵerenga uthenga wofunika wakuti [ŵerengani mutu wa Uthenga wa Ufumu]. Onani zimene ukunena pano patsamba 2 ponena za mavuto amene akuwonjezereka a . . . [ŵerengani mawu amene mwasankha mu Uthenga wa Ufumu]. Tikhulupirira kuti mudzasangalala ndi kuŵerenga uthenga wonse wapanthaŵi yake. Ili ndi kope lanu.”

12 Khalani ndi chikondwerero mwa aliyense amene alandira Uthenga wa Ufumu. Lankhulani modekha ndi momveka bwino; palibe chifuno chofulumizitsira ulaliki wanu. Tikufuna kufola gawo lathu bwino lomwe ndi kuona kuti onse amene asonyeza chifuno cha kuŵerenga Uthenga wa Ufumu apatsidwa kope lawolawo. Ngati panyumba palibe munthu, sonyezani bwino lomwe pa cholembapo za kunyumba ndi nyumba chanu kotero kuti mudzabwerenso panthaŵi yoyenera kudzagaŵira Uthenga wa Ufumu kwa mwininyumba. Uthenga wa Ufumu umenewu ungagwiritsiridwe ntchito mu umboni wa m’khwalala pamene munthu asonyeza chifuno cha kuŵerenga nkhaniyo. Makope ake sayenera kungoperekedwa kwa aliyense monga kuti anali mahandibilu. M’malo mwake, fikirani odutsawo, ndipo longosolani kufunika kwa uthenga umene ulimo. Gwiritsirani ntchito Uthenga wa Ufumu mu umboni wa mwamwaŵi, monga pamene muli paulendo, kapena pochitira umboni kwa antchito anzanu pa kupuma kwa masana. Aja amene ali obindikira mkati kapena osatulukira kunja angaugaŵire kwa anthu odzacheza, madokotala ndi manesi, amalonda, ndi ena amene amabwera kunyumba kwawo.

13 Kodi mudzachita maulendo obwereza angati mkati mwa mkupiti umenewu? Ochuluka ndithu, pakuti onse aja amene adzasonyeza chikondwerero mu Uthenga wa Ufumu ayenera kuwachezeranso. Paulendo woyamba, kuli bwino kusonyeza Uthenga wa Ufumu wokha. Ndiyeno, pamene mupitakonso, perekani ndemanga zingapo ponena za kukhala wapanthaŵi yake kwa Uthenga wa Ufumu. Mvetserani mosamalitsa pamene mwininyumba afotokoza lingaliro lake la zimene waŵerenga. Zokamba zake zidzakuthandizani kudziŵa zimene mudzasonyeza m’magazini atsopano ndipo mwinamwake mmene mungakonzekerere makambitsirano a mtsogolo. Ngati asonyeza kufuna paulendo wobwereza, yesani kuyambitsa phunziro Labaibulo.—1 Akor. 3:6, 7.

14 “Kuchititsa Kwanu Sikuli Chabe”: Kodi ntchito yonseyi idzaphula kanthu? Paulo anapereka chitsimikizo kwa Akorinto: “Kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.” (1 Akor. 15:58) M’kupita kwa zaka, zoyesayesa zathu za kugaŵira Uthenga wa Ufumu zadalitsidwa kwambiri. Okwatirana ena posamukira m’nyumba ina anapeza kope lakale la Uthenga wa Ufumu m’dirowa. Ndicho chinthu chokha chimene chinasiyidwa m’nyumbamo. Ataliŵerenga, anakambirana ndi mpingo wa kumaloko ndi kupempha phunziro Labaibulo. Anayamba kupezeka pamisokhano yonse ndiyeno pambuyo pake anatchula za chikhumbo chawo chofuna kubatizidwa. Mwinamwake kope limene musiyalo lingakhale ndi zotulukapo zofananazo!—Onani Awake!, November 8, 1976, tsamba 15.

15 Tili ndi ntchito yaikulu patsogolo pathupa. Chonulirapo chathu nchakuti mpingo uliwonse ufole gawo lake lonse pofika pa May 14 kapena pofika kumapeto a mweziwo ngati kuti kudzafuna kuwonjezera nthaŵi ya kugaŵira Uthenga wa Ufumu. Mitokoma yalinganizidwa mwa njira yakuti mpainiya wokhazikika ndi wothandiza aliyense alandire makope 100 a Uthenga wa Ufumu. Wofalitsa wa mpingo aliyense adzalandira makope mwina ofika ku 30. Ofalitsa ndi apainiya ayenera kulandira kokha makope amene adzakhoza kugaŵira ndipo ayenera kubweza otsalawo kuti ena awagwiritsire ntchito. Kugwirizana kwabwino pankhaniyi kudzatheketsa kugaŵira kwakukulu kwa uthenga wofunika umenewu. Ngati mipingo ina ilephera kumaliza kufola gawo lawo pofika pakati pa May chifukwa cha kukula kwa gawolo ndipo ngati makope adakalipo, kungakhale kothandiza kupempha mipingo ina yapafupi kuwathandiza. M’mipingo ina chosoŵacho chingakwaniritsidwe ndi mpingowo ngati ofalitsa awonjezera ntchito zawo mwa kulembetsa upainiya wothandiza kapena mwa kukhala ndi phande kaŵirikaŵiri mu utumiki.

16 Kudzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse kudzakhala kofunikira ngati titi tikwaniritse ntchito yathu. (Akol. 3:23) Miyoyo ili pangozi. Anthu sayenera kunyalanyaza tanthauzo la mikhalidwe ya dziko ya lerolino. Nthaŵi ikutha. Iwo ayenera kudziŵa choonadi chakuti munthu alibe njira yothetsera mavuto a dzikoli. Mulungu ali nawo. Aja amene akufuna kupeza madalitso a Mulungu ayenera kuchitapo kanthu mogwirizana ndi zofuna zake, ndipo ayenera kutero mosachedwa.

17 Kodi tikafika kumapeto a mkupiti wathu pa May 14, tidzagwetsa dzanja? Iyayi! Tidzakhalabe otanganitsidwa mogwirizana ndi uphungu wouziridwa wa Paulo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena