Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/00 tsamba 8
  • “Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu ndi Lotani?”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu ndi Lotani?”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Gaŵirani Uthenga wa Ufumu Na. 35 Kulikonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Tidzakhala ndi Ntchito Yapadera Kuyambira pa October 16 Mpaka pa November 12
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • “Akuchuluka m’Ntchito ya Ambuye”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Khalani “Achangu Pantchito Zokoma” m’April!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 10/00 tsamba 8

“Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu ndi Lotani?”

1 Anthu padziko lapansi akhala ndi funso limenelo. Ngakhale kuti anthu achita zambiri kwa zaka mazana ambiri, anthu athedwa nzeru chifukwa chakuti mavuto akuluakulu amene akhala akuvutitsa anthu kwa zaka masauzande akupitirirabe. (Yobu 14:1; Sal. 90:10) Kodi anthu angapeze kuti mpumulo?

2 M’miyezi ya October ndi November, tidzakhala ndi mwayi wapadera wouza anansi athu yankho la funso limenelo. Motani? Mwa kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36. Uli ndi mutu wakuti “Zaka 1000 Zatsopano—Kodi Tsogolo Lanu Ndi Lotani?” Milungu iŵiri yoyambirira m’mwezi wa October, tidzagaŵira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndiyeno kuyambira Lolemba pa October 16, mpaka Lachisanu pa November 17, tidzakhala pakalikiliki wogaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36. Pandaŵala imeneyi, m’kati mwa mlungu tizidzagaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36 wokha basi. Pamapeto a mlungu, tizidzagaŵira pamodzi ndi magazini atsopano.

3 Kodi Mudzachita Nawo Ndaŵala Imeneyi Mokwanira? Akulu, atumiki otumikira, ndi apainiya adzafuna kutsogolera ndaŵala imeneyi, popeza ndiwo akutsogolera ntchito. Ofalitsa ambiri asintha zochita zawo kuti achite upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena yonse iŵiri yogaŵira uthengawu. Ena akonza zothera nthaŵi yambiri kuposa imene amathera mu utumiki nthaŵi zonse.

4 Ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo angathandize kulimbikitsa aliyense wa m’gulu lawo kuchita nawo mokwanira ntchito yogaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36. Pangakhale ofalitsa ena amene afooka mu ntchito yolalikira. Akulu ayenera kuwayendera anthu ameneŵa n’kuona mmene angawathandizire. Mwina angakonze zakuti wofalitsa wozoloŵera ayendere limodzi ndi munthu aliyense wofooka m’munda m’miyezi imeneyi. Ulaliki wosavuta wa Uthenga wa Ufumu Na. 36 ungakhale womwe ukufunika polimbikitsa ofalitsa ameneŵa.

5 Umenewu udzakhalanso mpata wabwino kwa ophunzira Baibulo amene ali pafupi kutsiriza kuphunzira buku la Chidziŵitso ndipo akuyenera kukhala ofalitsa osabatizidwa kuyamba kuloŵa mu utumiki. Ngakhale ana angachite nawo ntchito yosangalatsayi.

6 Chimene chikufunika ndi ulaliki wosavuta basi. Munganene kuti:

◼ “Ndapatula nthaŵi yanga kuti ndithandize kugaŵira uthenga wofunika kwambiri uwu kubanja lililonse mu [tchulani dzina la mzindawo kapena la deralo]. Nali kope lanu. Chonde muliŵerenge.” Pogaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 36 kungakhale bwino kusatenga chikwama cha muulaliki.

7 Misonkhano Yokonzekera Utumiki Wakumunda Yolinganizidwa Bwino: Akulu ayenera kuonetsetsa kuti dongosolo lochitira umboni ndi loyenera komanso n’lothandiza. Makamaka woyang’anira utumiki ayenera kuonetsetsa kuti pali gawo lalikulu la kunyumba ndi nyumba ndiponso la m’malo amalonda kuti aliyense achite nawo mokwanira ntchito imeneyi. Ngati n’kotheka, misonkhano yokonzekera utumiki iyenera kukhalako tsiku lililonse m’kati mwa mlungu, ndiponso pamapeto a mlungu. Pangakhale dongosolo lokumana chakumadzulo kuti ana asukulu, ogwira ntchito zamashifiti, ndi ena adzapezekepo.

8 Zoyenera Kuchita pa Nyumba Zimene Sitinapeze Anthu: Cholinga chathu n’chakuti tilankhulane ndi eninyumba ambiri mmene tingathere. Ngati panyumba imene mwafikapo palibe munthu, lembani nambala ya nyumbayo ndipo pitaniko nthaŵi ina. Ngati podzafika mlungu womaliza ndaŵalayi simukupezapobe eninyumba, mungawasiyire kope la Uthenga wa Ufumu Na. 36 pamalo obisika kwa anthu odutsa. Pogaŵira m’madera akumidzi ndiponso m’gawo lalikulu loti silingafoledwe m’nthaŵi ya ndaŵalayo, akulu angalangize mpingo kusiya kope la Uthenga wa Ufumu Na. 36 paulendo woyamba panyumba zimene sanapeze anthu.

9 Tiyeni Tikhale Pakalikiliki! Mipingo iyenera kuyesetsa kufola magawo awo ndaŵalayi isanathe pa November 17. Ngati gawo lanu lili lalikulu kwambiri, ofalitsa ena angayende okha ngati angathe komanso ngati sipangakhale vuto. Zimenezi zidzapangitsa kuti tifikire anthu oyenerera ambiri mmene tingathere. Onetsetsani kuti mwalemba ndi kusunga bwinobwino mayina a anthu onse osonyeza chidwi.

10 Akulu ayenera kuona chiŵerengero cha magazini owonjezera chimene mpingo ungafune ndipo ayenera kuoda mogwirizana ndi zimenezi. Simuyenera kuoda Uthenga wa Ufumu Na. 36, popeza tatumiza kumpingo uliwonse. Apainiya apadera, okhazikika, othandiza, ndi ofalitsa adzalandira makope 50 aliyense kuti agaŵire. Choncho kodi mwakonzeka ndipo kodi muli okonzeka kudzatanganidwa m’ntchito yapadera imeneyi? Ndife amwayi zedi kudziŵitsa anansi athu zimene Mulungu walonjeza kuti zichitika posachedwa pompa!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena