Tidzakhala ndi Ntchito Yapadera Kuyambira pa October 16 Mpaka pa November 12!
1 “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!” Umenewu ndi mutu wa Uthenga wa Ufumu Na. 37, womwe udzagawidwe pa dziko lonse lapansi kuyambira mwezi wamawa. Milungu iwiri yoyambirira ya mwezi wa October, tidzagawira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kuyambira Lolemba pa October 16, mpaka Lamlungu pa November 12, tidzakhala pa kalikiliki kugawira Uthenga wa Ufumu Na. 37. Loweruka ndi Lamlungu pa nthawi ya ntchito yapaderayi, tizidzagawira Uthenga wa Ufumu Na. 37 limodzi ndi magazini atsopano.
2 Ndani Angachite Nawo?: Aliyense amene ali wofalitsa wa uthenga wabwino adzafuna kuchita nawo ntchitoyi mokwanira. Ena akhoza kudzachita upainiya wothandiza. Kodi muli ndi ana kapena ophunzira Baibulo amene akupita patsogolo mwauzimu? Athandizeni kuti alankhulane ndi akulu kuti aone ngati akuyenerera kukhala ofalitsa osabatizidwa. Akulu akalankhule ndi ofalitsa osalalikira kuti akawalimbikitse kugwira nawo ntchitoyi, ndipo mwina akhoza kumalalikira limodzi ndi ofalitsa ena odziwa bwino kulalikira.
3 Tikutumiza timapepala ta Uthenga wa Ufumu Na. 37 ku mipingo yonse n’cholinga choti ofalitsa ndi apainiya athe kulandira timapepala tosachepera 30. Anthu achidwi amene si ofalitsa akhoza kulandira timapepala tisanu kuti adzapatse achibale awo ndi anzawo. Ofalitsa onse adzasunge nambala ya timapepala tomwe apereka kwa anthu n’kudzalemba nambalayi kuseri kwa malipoti awo a utumiki kumapeto kwa mwezi wa October ndi November. Mlembi adzawerengetsera timapepala tonse tomwe mpingo wagawira kwa anthu ndipo adzatumiza nambala imeneyi ku ofesi ya nthambi kumapeto kwa miyezi iwiriyi. Timapepala tilitonse ta Uthenga wa Ufumu tomwe tidzatsale ntchito yapaderayi ikadzatha tikhoza kugwiritsidwa ntchito mu utumiki wa mtundu wina uliwonse.
4 Zomwe Munganene: Nenani mawu ochepa chabe, kuti muthe kuuza anthu ambiri uthengawu. Mukhoza kunena kuti: “Ndikugwira nawo ntchito yothandiza anthu yomwe ikuchitika padziko lonse lapansi, yowauza uthenga wofunika uwu. Tengani kapepala aka mukawerenge.” Zingakhale bwino mutati musatenge chikwama choikamo mabuku popita ku ulaliki. Onetsetsani kuti mukulemba maina a anthu onse amene asonyeza chidwi.
5 Momwe Mungalalikirire M’gawo Lanu Lonse: M’malo mogawira Uthenga wa Ufumu mu msewu, yesetsani kulalikira m’gawo lanu lonse lomwe mungakwanitse, la kunyumba ndi nyumba ndi la malonda. Lembani nyumba zonse zomwe simunapezeko anthu, ndipo yesetsani kudzabwererako pa nthawi yosiyana kapena pa tsiku losiyana la pamlungu. Kuyambira Lolemba pa November 6, mukhoza kusiya timapepalati pa nyumba zonse zomwe simunapezepo anthu. Komabe, ngati mpingowo uli ndi gawo lalikulu kwambiri loti sungathe kulikwanitsa lonse pa nthawi imene tapatsidwayi, akulu angakonze zoti Uthenga wa Ufumu uzisiyidwa pa nyumba zomwe simunapezepo anthu pa nthawi yonse ya ntchito yapaderayi.
6 Kuwonongedwa kwa ‘Babulo Wamkulu’ kwayandikira kwambiri. Anthu akufunika kuchokamo Babulo Wamkuluyo asanawonongedwe kotheratu. (Chiv. 14:8; 18:8) Konzekeranitu panopa kuti mudzathe kugwira nawo mokwanira ntchito yapadera yapadziko lonse imeneyi, youza anthu onse kuti mapeto a chipembedzo chonyenga ayandikira.