Tidzakhala ndi Ntchito Yapadera Yogawira Kapepala Kuyambira pa October 20 Mpaka pa November 16
1 Kwa milungu inayi, kuyambira Lolemba, pa October 20, tidzayamba ntchito yapadera yogawira kapepala katsopano ka mutu wakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Sitikukayikira kuti ntchito ya padziko lonse imeneyi idzathandiza anthu ambiri kukhala ndi chidwi chofuna kudziwa kumene angapeze choonadi.—Yoh. 17:17.
2 Kapepalaka kali ndi mayankho a m’Baibulo osavuta kumva a mafunso 6 ofunika kwambiri. Mafunsowa ndi akuti: “Kodi Mulungu amatiganiziradi?” “Kodi nkhondo ndi kuvutika zidzathadi?” “Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?” “Kodi akufa adzauka?” “Kodi ndingatani kuti Mulungu aziyankha mapemphero anga?” ndi “Kodi ndingatani kuti ndikhale ndi moyo wosangalala?” Matchalitchi Achikristu sayankha mokhutiritsa mafunso amenewa. Anthu ambiri amene si Akhristu amafunsanso mafunso amenewa, ndipo sadziwa kuti Baibulo lili ndi mayankho omveka bwino. Sitikukayikira kuti uthenga umenewu udzakhudza anthu ambiri.
3 Folani Gawo Lanu: Mudzayesetse kufola gawo lanu lonse mwa kulalikira nyumba ndi nyumba. Ngati muli ndi gawo lalikulu, akulu angadzakuuzeni kuti mudzasiye kapepala panyumba imene simunapeze anthu paulendo woyamba womwewo. Kumbukirani kupatsa kapepala anzanu oyandikana nawo, achibale anu, anzanu akusukulu kapena akuntchito, ndi ena amene mumakonda kucheza nawo. Mwina mungakonze zodzachita upainiya wothandiza m’mwezi wa October kapena November. Kodi muli ndi mwana kapena wophunzira Baibulo wopita patsogolo mwauzimu amene angayenerere kugwira nawo ntchitoyi monga wofalitsa wosabatizidwa? Ngati ndi choncho, dziwitsani akulu.
4 Zimene Munganene: Kuti tifikire anthu ambiri ndi uthengawu, ndi bwino kulankhula mwachidule. Funsani eninyumba funso limodzi pa mafunso 6 omwe ali patsamba loyamba la kapepalako, kenako asonyezeni yankho lake mu kapepalako. Njira imeneyi idzathandiza ofalitsa onse kukonza ulaliki wawo mogwirizana ndi gawo lawo. Ngati mwaona kuti munthu wina ali ndi chidwi, lembani ndipo mudzabwerereko. Loweruka ndi Lamlungu mungagawire magazini atsopano limodzi ndi kapepalako. Ntchitoyi ikadzatha pa November 16, tidzagawira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Timapepala totsala tidzagawiridwa monga timapepala tina tonse.
5 Yambitsani Phunziro la Baibulo: Cholinga chachikulu cha kapepalaka ndicho kutithandiza kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Pamene mukubwerera kwa munthu amene anasonyeza chidwi, mungamufunse kuti akuuzeni mfundo ya m’Baibulo imene inamulimbikitsa kapena kumukhudza kwambiri. M’sonyezeni tsamba lomaliza limene likufotokoza za phunziro la Baibulo, ndipo m’patseni buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ngati n’kotheka, kambiranani mwachidule ndime imodzi kapena ziwiri pamutu umene ukufotokoza mwatsatanetsatane nkhani imene iye anatchula.
6 Yehova akufuna anthu amene angam’lambire “ndi mzimu ndi choonadi.” (Yoh. 4:23) Tonsefe tikulimbikitsidwa kugwira nawo ntchito yapadera imeneyi, yothandiza ena kudziwa choonadi.