Gaŵirani Uthenga wa Ufumu Na. 35 Kulikonse
1 October Ndi November Ikhala Miyezi Ya Kalikiliki Kwambiri Kwa Tonsefe. M’masiku 11 Oyamba A October, Tidzagaŵira Makope A Nsanja Ya Olonda Ndi A Galamukani! Ndiyeno, Kuyambira Lamlungu, October 12, Mpaka Lamlungu, November 16, Tidzaloŵa Nawo Pakugaŵira Uthenga Wa Ufumu Na. 35 Kumene Kukuchitika Padziko Lonse, Udzakhala Mwaŵi Wathu Kukafikitsa Uthenga Wofunika Umenewu Kwa Anthu Onse A M’dera Lathu. Ndiwo Yankho La Funso Lakuti, “Kodi Anthu Onse Adzakondanapo?” Pamkupiti Wapadera Umenewu, Tidzagaŵira Uthenga Wa Ufumu Na. 35 M’masiku A Mkati Mwa Mlungu. Kumapeto Kwa Mlungu, Kuphatikiza Pa Kugaŵira Uthenga Wa Ufumu, Tidzagaŵiranso Magazini Atsopano.
2 Kodi Ndani Angatengemo Mbali? Monga mwa nthaŵi zonse, akulu ndiwo adzatsogolera pantchitoyi. Aliyense amakondwa nako kugaŵira Uthenga wa Ufumu, ndipo mosakayikira ofalitsa ambiri adzalembetsa upainiya wothandiza kwa mwezi umodzi kapena miyezi yonse iŵiri ya mkupitiwo. Ofalitsa ena adzafuna kuthera maola ambiri mu utumiki kuposa nthaŵi zonse.
3 Kodi muli ndi wophunzira Baibulo yemwe wapita patali ndi phunziro lake m’buku la Chidziŵitso koti posachedwapa angayenerere kumaloŵa mu utumiki wakumunda? Mwina posachedwapa angadzakhale wofalitsa wosabatizidwa koti angadzaloŵe nawo mumkupiti wa Uthenga wa Ufumu. Pangofunika ulaliki wachidule posonyeza trakitilo. Mwachitsanzo, munthu anganene kuti: “Uthengawu ngwofunika kwambiri koti ukufalitsidwa padziko lonse mwezi uno m’zinenero 169. Ndingakonde kuti mukhale ndi kope lanulanu.” Ngakhale ana aang’ono angathandize pantchito yosangalatsa imeneyi.
4 Ochititsa phunziro la buku ayenera kulimbikitsa munthu aliyense wa m’kagulu kawo kuti agaŵire nawo mokwanira Uthenga wa Ufumu Na. 35. Pangakhalenso ofalitsa ena amene anafooka koma omwe angayambenso kuchita utumiki mutawalimbikitsa. Mkupitiwo usanayambike, akulu ayenera kukachezera aliyense wa amenewo kuti aone zimene angachite powathandiza kutsagana ndi ofalitsa aluso mu utumiki umenewu.
5 Kodi Tingakumane Liti Popita ku Utumiki? Ntchito yonseyi idzafuna makonzedwe abwino ndi otheka a kuchitira umboni monga gulu. Ngati nkotheka, tizikonzekera kukumana kwa utumiki tsiku lililonse la mlungu, pakutha kwa mlungu, ndi madzulo. Kukumanako kuzikhala panthaŵi zimene zidzatheketsa ofalitsa ndi apainiya kugwiritsira ntchito mokwanira nthaŵi ya kuchitira umboniyo. Tingakonze kuti tizikumananso chakumasana kuchitira ana a sukulu, ogwira ntchito zashifiti, ndi enanso. Woyang’anira utumiki ayenera kutsimikiza kuti pali gawo lalikulu la nyumba ndi nyumba ndi malo a ntchito kuti aliyense akhale ndi mbali yokwanira pantchitoyi. Ngati dera lina lili ndi ofalitsa ambiri, ayenera kusamala kuti ndi anthu angati omwe akugwira ntchito m’kachigawo kena ka gawolo.
6 Bwanji Ngati Panyumba Sitipezapo Anthu? Tikufuna kulankhula mwachindunji ndi eni nyumba ambiri, kuti tiwafotokozere chifukwa chimene ayenera kuŵerengera Uthenga wa Ufumu Na. 35. Choncho ngati panyumba pamene mwafikapo palibe munthu, lembani keyala ndipo mubwererepo panthaŵi ina. Ngati mwalephera kuonana ndi eni nyumbawo, podzafika mlungu womaliza wa mkupitiwu, mungasiye kope la Uthenga wa Ufumu pakhomo pamalo omwe odutsa sangalione. M’madera okhala anthu, muzikhala okonzekera kupereka Uthenga wa Ufumu kwa omwe angakhale akuyenda mumsewu. Ngati tikugwira ntchito m’madera a kumidzi ndi kumene kuli gawo lalikulu loti silingafoledwe m’nthaŵi ya mkupitiwu, tingasiye kope la Uthenga wa Ufumu panyumba popanda anthu ngakhale kuti nkuyamba kufikapo.
7 Kodi Cholinga Chathu Nchiyani? Mipingo iyenera kuyesetsa kugwiritsira ntchito makope awo onse a Uthenga wa Ufumu pofola gawo lawo mkupitiwu usanathe pa November 16. Ngati gawo la mpingo wanu lili lalikulu ndithu ndipo ngati palibe vuto kugwira ntchito nokha m’malo mwa kukhala ndi mnzanu, mungathe kupita nokha. Zimenezo zidzakuthandizani kufikitsa uthenga wabwino kwa anthu ambiri oyenera. (Mat. 10:11) Mungachite bwino kutenga matrakiti angapo m’manja ndi Baibulo m’thumba mwanu kapena m’kachikwama, m’malo mwa m’chola. Tsimikizani kuti mwalemba bwinobwino keyala ndi dzina la anthu amene anasonyeza chidwi.
8 Kodi Mwakonzeka Kuyamba? Akulu ayenera kudziŵiratu kuti ndi magazini angati owonjezera omwe mpingo ungafune ndipo ayenera kuoda mogwirizana ndi mmene angafunire. Simufunikira kuchita kuoda Uthenga wa Ufumu Na. 35, popeza tikutumizira mpingo uliwonse mtokoma wake. Apainiya apadera, okhazikika, ndi othandiza aliyense adzakhala ndi makope 250 ogaŵira, koma ofalitsa a mpingo adzalandira makope 50 aliyense. Ntchito yomwe tapatsidwa ndi yomweyi. Kodi mukufunitsitsa kuchita nawo ntchito yosangalatsayi? Mosakayikiradi mukufuna. Tiyenitu tifalitse konsekonse uthenga wofunika wa m’Baibulo womwe uli mu Uthenga wa Ufumu Na. 35!