Khomo Lalikulu Loloŵera Kuntchito Nlotseguka
1 Monga wolalikira uthenga wabwino wachangu, Paulo anafufuza madera omwe anasoŵa kwambiri alaliki, limodzi la iwo linali mzinda wa Efeso. Polalikira kumeneko, ulaliki unamuyendera bwino kwambiri moti analembera Akristu anzake kuti: “Panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa.” (1 Akor. 16:9) Paulo anatumikirabe m’dera limenelo ndipo anathandiza Aefeso ambiri kukhala okhulupirira.—Mac. 19:1-20, 26.
2 Lero, khomo lalikulu loloŵera kuntchito latitsegukira. Tikupemphedwa kuthandiza mipingo imene sikwanitsa kufola gawo lawo lonse chaka ndi chaka. Choncho mwa khama lathu tingathandize madera ena amene ali osoŵa.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 8:13-15.
3 Kodi Mungatumikire Kumene Kuli Kusoŵa Kwakukulu? Kodi mumasinkhasinkha mwa pemphero ngati mungathe kukatumikira kwina? Mwinanso simungafunikire kusamuka ngati pali mpingo wina wofuna thandizo mumzinda wanu womwewo. Bwanji osalankhula ndi woyang’anira dera za nkhaniyo mumve zimene anganene? Kapena zingachitike kuti m’dera lomwelo la mpingo wanu, muli anthu ambiri ogontha kapena a chinenero china omwe sanathandizidwepo ndi wina aliyense. Kodi mungayesetse kuphunzira chinenero chawocho kuti muwathandize? Mwinanso pali kale anthu a chinenero china kapena mpingo womwe wakhala ‘ukupempha Mwini kututa kuti akokose antchito ena a Ufumu.’ (Mat. 9:37, 38) Ngati zili choncho, kodi mungapite?
4 Zaka makumi angapo zapitazo, mabanja achikristu zikwi zambiri anasamukira kumaiko ena kuti akachite mbali yaikulu pantchito yotuta. Mwamuna wina ndi mkazi wake omwe anachita zimenezo anati: “Tinafuna kutumikira Yehova kumene tikanatha kuchita zochuluka kwenikweni.” Ngati muli ndi chikhumbo chimenechi ndipo mukuona kuti mungathe kusamukira kwina m’dziko mommuno, kapena ngati muli woyeneretsedwa kukatumikira kudziko lina, choyamba kambitsiranani zolinga zanu ndi akulu a mumpingo wanu.
5 Ngati mukufuna kufunsira ku Sosaite kuti mudziŵe kumene kuli kusoŵa, lemberani kalata Komiti Yautumiki Yampingo, mulongosolemo chikhumbo chanucho. Adzaphatikizapo ndemanga zawo pakalatayo ndi kuzitumiza pamodzi ku Sosaite. Mulimonse mmene zingakhalire, malinga ngati khomo lalikulu loloŵera kuntchito likali chitsegukire, tonsefetu tikhalebe otanganidwa mu utumiki wa Yehova.—1 Akor. 15:58.