Kodi Mpingo Wanu Uli ndi Gawo Lalikulu?
1 Yesu analalikira mokwanira mu gawo lalikulu la Israyeli wakale, kuyambira ku mizinda ya ku Yudeya mpakana ku midzi ya ku Galileya. (Marko 1:38, 39; Luka 23:5) Ifenso tiyenera kufotokoza uthenga wabwino kwa anthu ambiri mmene tingathere. (Marko 13:10) Komabe, zimenezi n’zovuta. Chifukwa?
2 Chifukwa chakuti m’Malaŵi muno magawo a mipingo yambiri ndi osafoledwa. Kodi tingatani kuti tithandize anthu a m’magawo akuluakulu ameneŵa kuphunzira zenizeni ponena za Yehova, Yesu ndi Ufumu?
3 Konzekerani Bwino: Kuti zinthu ziyende bwino kwambiri, woyang’anira utumiki ndi mtumiki wosamalira magawo afunika kuyang’anira ntchito ya mpingo. Mwina angapatule masiku ena a Loŵeruka kapena lina lililonse amene anthu ambiri angathe kulalikira tsiku lonse. Pokalalikira m’magawo akutali, konzekerani zokhala nthaŵi yambiri yatsikulo mu utumiki wakumunda ngati mungathe. Mungachite mofulumirirapo msonkhano wokonzekera utumiki kusiyana ndi masiku onse kuti mukhale ndi nthaŵi yoyenda kupita ku gawolo. Kapenanso mungakachitire msonkhanowo pafupi ndi dera limene mukalalikirelo.
4 Konzani magawo kuti gulu limene likulalikira lipite ku nyumba zonse m’dera limenelo. Onetsetsani kuti mwatenga mabuku okwanira. Ngati gawolo simulalikirako pafupipafupi, ndibwino kusiya thirakiti kapena magazini yakale panyumba imene simunapezepo anthu. Ngati muli ndi thirakiti lakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? m’chinenero chanu, ligaŵireni kwa aliyense amene mukumane naye ndiponso siyani limodzi panyumba imene simunapeze anthu.
5 Gwirani Ntchito Mogwirizana Kwambiri: Kuti tilalikire mu gawo lalikulu m’pofunika kuti mpingo wonse uchite zinthu mogwirizana. M’pofunika kuchita zinthu mwanzeru mukapeza eninyumba amene akufunitsitsa kulankhula nanu. Musaiŵale kuti pakufunika kufikira anthu onse m’gawolo, ndiponso lingalirani anthu a gulu lanu. Ngati mukufuna kupitiriza kukambirana ndi munthu wachidwi kwa nthaŵi yaitali, onetsetsani kuti gulu linalo likupitiriza utumiki wakumunda.
6 Pangani makonzedwe enieni odzapitanso kwa anthu achidwi. Mukatenga dzina la munthu wachidwi, tenganinso adiresi yake kuti mwina mungapitirize kumulalikira mwa kumulembera kalata.
7 Tili ndi mwayi zedi kutsatira malangizo a Yesu, akuti: “Mu mzinda uliwonse, kapena m’mudzi mukaloŵamo, mufunsitse amene ali woyenera momwemo.” (Mat. 10:11) Ndithudi Yehova adzadalitsa ntchito yanu mukadzipereka kugwira ntchito yopindulitsayi.