Tikapanda Kupeza Anthu Panyumba
1. Kodi timakumana ndi vuto lanji tikamalalikira khomo ndi khomo?
1 M’madera ambiri zikuvuta kupeza anthu panyumba. “Nthawi yovuta” ino, ambiri amagwira ntchito maola ochuluka kuti adzipezere zofunika pamoyo. (2 Tim. 3:1) Ena amakhala ali ku ntchito kapena kokamwaza ndalama kapenanso kokasangalala ndi moyo, ndipo sakhala panyumba. Kodi tingawapeze bwanji anthu amenewa kuti tiwauze uthenga wabwino?
2. Kodi tingachite chiyani kuti tionetsetse kuti anthu omwe sitinawapeze pa nyumba akusamalidwa?
2 Muzilemba Ngati Simunapeze Anthu: Choyamba tiyenera kulemba ngati sitinapeze anthu panyumba inayake. Zimenezi ndi zofunika kwambiri ngati mumalowa m’gawo lanu mobwerezabwereza. Kodi mumalemba dzina la msewu, nambala ya gawo, dzina lanu, ndi deti pa fomuyo? Mungasiyepo mpata pafomuyo wodzalembapo ngati inuyo kapena wofalitsa wina wabwererakonso kapena podzayendera nyumba zimene simunapezeko anthu. Mukamaliza kulalikira gawo lanu, kumbukirani zokapereka zimene mwalembazo kwa munthu amene amasunga khadi la magawo. Koma ngati wakulolani kupitanso kwa anthu amene simunawapeze pa nyumba, musam’patse fomuyo ndi zilizonse zimene mwalemba. Gwiritsani ntchito pepala lina kulembapo anthu achidwi amene mudzafuna kuwapitiranso.
3. Kodi zinthu zina zimene mungachite kuti mupeze anthu amene poyamba simunawapeze pa nyumba ndi zotani?
3 Yesani Nthawi Ina: Mwina amene sanapezeke pa nyumba m’kati mwa mlungu angathe kupezeka madzulo kapena Loweruka ndi Lamlungu. Kodi mungakonze zowapitira anthu amenewa nthawi yabwino? (1 Akor. 10:24) Ngati simungakwanitse, mungachite bwino kuuza wofalitsa wina amene angapiteko nthawi ina kuti akaonane ndi anthu amene sanali pa nyumbawo. Apo ayi, mungawalembere kalata kapena kuwaimbira foni. Ofalitsa amene sangakwanitse kupita ku ulaliki wa khomo ndi khomo chifukwa cha kudwala angakonde kukuthandizani kuchita zimenezi.
4. N’chiyani chikusonyeza kuti ndi bwino kuyesetsa kukaonana ndi anthu amene sitinawapeze pa nyumba?
4 Pali nkhani ina imene ikusonyeza kufunika koyesetsa kuonana ndi anthu amene sitinawapeze pa nyumba. Ofalitsa anapita mobwerezabwereza kunyumba ina kwa zaka zitatu osapezako munthu, koma kenako anapezako munthu. Iwo anapeza kuti munthuyo nthawi yonseyo anali kudikirira wa Mboni kuti adzayambirenso kuphunzira naye Baibulo ngati mmene ankachitira asanasamukire m’deralo.
5. Kodi ndi liti pamene tinganene kuti gawo lathu talimaliza?
5 Malizani Gawo: Kodi ndi liti pamene tinganene kuti gawo lathu talimaliza? Pamene tachita zonse zotheka kuti tionane ndi munthu panyumba iliyonse. Mwina ndi bwino kusiya kapepala kapena magazini akale mwanzeru panyumba pomwe palibe anthu, makamaka m’magawo omwe sapitidwapitidwa. Gawo liyenera kumalizidwa pa miyezi inayi. Kenako mtumiki wa magawo ayenera kuuzidwa mwachangu kuti alembe zimenezi m’faelo yake.
6. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kulalikira uthenga wabwino kwa aliyense m’gawo lathu?
6 Tikufuna kuti anthu ambiri akhale ndi mwayi wophunzira kuitana pa dzina la Yehova kuti adzapulumuke. (Aroma 10:13, 14) Enanso mwa anthu amenewa ndi monga aja amene sitiwapeza pakhomo tikamalalikira nyumba ndi nyumba. Mofanana ndi mtumwi Paulo, cholinga chathu chikhale “kuchitira umboni bwino lomwe za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu.”—Mac. 20:24.