Kodi Nkusungiranji Cholepambo cha osapezeka Panyumba?
1 Tsiku lina mmamaŵa banja lina la Mboni linali mu utumiki wakumunda. Pambuyo pake tsiku lomwelo, iwo anabwerera kukaonana ndi anthu amene sanapeze panyumba m’ndime yawo. Mwamuna wina anawaloŵetsa m’nyumba namvetsera kwambiri. Anatenga buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha napempha kuti Mbonizo zikabwerenso. Iye anali asanalankhulepo ndi Mboni za Yehova ndipo anali ndi mafunso ambiri amene anafuna mayankho ake; phunziro la Baibulo linayambitsidwa. Banja limeneli linakondwera kwambiri kupeza munthu wonga nkhosa ameneyo. Kodi mukufuna kukhala ndi chokumana nacho chonga chimenecho? Kusunga cholembapo chabwino cha osapezeka panyumba ndi kubwererako mwamsanga kungakutheketseni kupeza zotero.
2 Talimbikitsidwa nthaŵi zambiri kusunga cholembapo cholondola cha osapezeka panyumba ndi kupitako kachiŵirinso mwamsanga. Monga momwe chokumana nachochi chikusonyezera, ulendo wina patsiku lomwelo ungatulutse zinthu zabwino kwambiri. Pamene kuli kwakuti tingakhale ndi cholinga cha kufola ndime yathu, mwinamwake tingakhale osasamala kwambiri za kusunga cholembapo cha aja osapezeka panyumba. Ena amati: ‘Timafola ndime yathu kamodzi pa milungu iŵiri kapena itatu iliyonse; palibe chifukwa chosungira cholembapo chotero popeza kuti ndi iko komwe tidzabwererako mwamsanga.’ Komatu zimenezo zimatipatsa zifukwa zinanso zosungira cholembapo. Kumene ndime imafoledwa kaŵirikaŵiri, kupitanso kwa amene sapezeka panyumba kumatikhozetsa kusasiya aliyense pofunafuna oyenerera. Motani?
3 Kumadera ambiri, nzika zake zokwanira 50 peresenti kapena kuposapo samakhala panyumba masana. Chotero, mwanjira ina, timafutukula ndime yathu mwa kusumika maganizo kwambiri pa osapezeka panyumba. Ngakhale ngati ndime siimafoledwa kaŵirikaŵiri, tingakhale ndi zotulukapo zabwino pamene tiyesayesa kufikira aliyense tisanasonyeze kuti ndimeyo inafoledwa.
4 Nthaŵi zambiri mungalinganize kufikira osapezeka panyumba pa tsiku lina, makamaka mkati mwa mlungu womwewo. Ambiri amaona bwino kupitako pa tsiku lina ndi nthaŵi ina yosiyana ndi ija ya poyamba. Mwina mungasankhe kugwiritsira ntchito nthaŵi ina pa Loŵeruka kapena pa Sande kupita kwa osapezeka panyumba amene munalemba mumlunguwo. Ndiponso, mipingo yambiri yapeza kuti kupanga maulendo otero madzulo kukali koyera kwakhala kobala zipatso. Mwina amapeza theka la anthu akumaloko ali panyumba.
5 Muyenera kulemba maulendo obwereza pa zolembapo zanu. Ngati simukhoza kubwerera kunyumba imene panalibe munthu, muyenera kupatsa cholembapo chanu cha osapezeka panyumba kwa mbale wotsogolera kaguluko, kuti chidzagwiritsiridwe ntchito ndi kagulu kamene kakupita m’gawolo.
6 Kusamalira kwambiri mbali imeneyi ya utumiki wathu kungawonjezere kubala zipatso kwathu ndiponso chimwemwe chathu. Kungatipatse chikhutiro chimene chimadza chifukwa cha kudziŵa kuti sitinasiye aliyense pofunafuna ndi posamalira onga nkhosa.—Ezek. 34:11-14.