Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/95 tsamba 4
  • Uthenga Wabwino wa Ofatsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Uthenga Wabwino wa Ofatsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Gaŵirani Magazini Nthaŵi Iliyonse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Yesetsani Kukhala Ofatsa Kuti Muzisangalatsa Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 5/95 tsamba 4

Uthenga Wabwino wa Ofatsa

1 Tikukhala ndi moyo panthaŵi imene chiweruzo chili pafupi kwambiri. (Ezek. 9:5, 6) Nkofunika kufulumira kuti anthu kulikonse adziŵe kotero kuti akonzekere zimene zilinkudza. Mwa kukoma mtima kwake, Yehova watumiza anthu ake kuti ‘akalalikire mawu abwino kwa ofatsa.’ (Yes. 61:1, 2) Magazini athu amatithandiza kulengeza uthenga wabwino umenewu kulikonse.

2 Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! amapereka chakudya chotafuna chauzimu chimene chimatilimbitsa ndi kutisonkhezera. Nsanja ya Olonda imatonthoza ofatsa ndi uthenga wabwino wakuti posachedwa Ufumu wa Mulungu udzasandutsa dziko lapansi paradaiso. Galamukani! amakulitsa chidaliro m’lonjezo la Mlengi la dziko latsopano lamtendere ndi losungika. Kugaŵiridwa kwambiri kwa magazini ameneŵa ndiko njira yamwamsanga koposa yoperekera uthenga wabwino kwa ofatsa. Kodi ndi mfundo zokambitsirana zotani zimene tingasonyeze m’makope atsopano?

3 Mukhoza kugaŵira “Nsanja ya Olonda” ya May 1 mwa kusonyeza nkhani yakuti “Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku” ndi kufunsa funso lotsatirali:

◼ “Kodi muganiza kuti ndi phindu lotani limene tingapeze mwa kuŵerenga Baibulo? [Yembekezerani yankho.] Baibulo lokha, pa Aroma 15:4, limatithandiza kuyankha funsolo. [Ŵerengani Aroma 15:4.] Kwathu kuno anthu ambiri ali ndi Baibulo, koma ndi oŵerengeka chabe amene amapeza nthaŵi ya kuliŵerenga. Tikhulupirira kuti chiyembekezo chokha chotsimikizirika cha mtsogolo chimapezeka m’Baibulo, ndipo tidzadala ngati tiliŵerenga.” Kambanipo mawu ena oyenera, ndiyeno gaŵirani magaziniwo ndi kuwafotokozera za sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda.

4 “Nsanja ya Olonda” ya May 15 ili ndi nkhani yochititsa chidwi yakuti: “Moyo Watsopano wa Makolo Athu Akufa.” Mwina mungakhoze kukopa munthu ndi mawu oyamba otsatirawa:

◼ “Anthu ambiri kaŵirikaŵiri amafuna kudziŵa kuti makolo awo akufa anali otani. Popeza kuti anafa ndipo kulibeko, anthu ochuluka amati sitidzawadziŵa. Kodi muganiza kuti tikhoza kudzawaona makolo athu akufa?” Yembekezerani yankho. Ŵerengani Yohane 5:28, 29, ndi kufotokoza mmene Mulungu walonjezera kuwapatsa moyo watsopano m’dziko lapansi la paradaiso. Gaŵirani sabusikripishoni.

5 Mungagaŵire “Galamukani!” wa May 8 mwa kufunsa funsoli:

◼ “Kodi muganiza kuti pafunikira chiyani kuti moyo ukhaledi watanthauzo?” Yembekezerani yankho. Sonyezani nkhani yakuti “Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani?”, patsamba 29, ndipo ŵerengani mawu a Solomo pa Mlaliki 2:11. Ndiyeno, tchulani uphungu wake pachaputala 12, vesi 13. Uzani mwininyumba kulandira magaziniwo.

6 Ngati mukugaŵira magazini May 14 asanafike, musaiŵale kunyamula makope a Uthenga wa Ufumu Na. 34. ndi kuwagaŵira kwa aliyense amene sanalandire kopelo. Nthaŵi zonse tiyenera kukhala okonzekera kugaŵira ena mabuku athu, pozindikira kuti ena m’banja, limodzinso ndi mabwenzi amene angawachezere angawaŵerenge. (1 Tim. 6:18) Uthenga wabwino umene timapereka kwa ofatsa ungapulumutse miyoyo yawo.—1 Tim. 4:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena