Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 10/95 tsamba 8
  • Gaŵirani Magazini Nthaŵi Iliyonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gaŵirani Magazini Nthaŵi Iliyonse
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Gwiritsirani Ntchito Magazini Athu m’Njira Yabwino Koposa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Khalani Ofunitsitsa Kugaŵira sabusikripishoni Mu October
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
  • Magazini Amalengeza Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 10/95 tsamba 8

Gaŵirani Magazini Nthaŵi Iliyonse

1 Tili ndi chifukwa chabwino chothokozera Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kodi ndi magazini ena ati omwe amakopa anthu padziko lonse? Mwezi uno tidzagwiritsira ntchito magaziniwo m’ntchito yathu yolalikira, ndipo makope a October ali ndi chidziŵitso champhamvu chotani nanga! Nthaŵi zambiri, timagaŵira magazini athu ochuluka m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba; komabe, tidzafunikira kukhalanso okonzeka kugaŵira masabusikripishoni nthaŵi iliyonse yoyenera.

2 Pogaŵira “Nsanja ya Olonda” ya October 1, mungadzutse chidwi pa nkhani yakuti “Dziko Lopanda Nkhondo—Lidzafika Liti?” mwa kunena kuti:

◼ “Anthu ambiri amadabwa kuti nchifukwa ninji dziko lopanda nkhondo lioneka kukhala losatheka ngakhale kuti anthu akuyesayesa ndithu. Kodi muganiza bwanji za mawu aŵa patsamba 5 mu Nsanja ya Olonda ya October 1? [Ŵerengani masentensi oyamba m’ndime ziŵiri zoyamba pansi pa kamutu kakuti “Chipembedzo—Chopinga Chachikulu,” ndipo yembekezani yankho.] Ndithudi, zimenezi sizikutanthauza kuti nkhondo zidzapitiriza kukhalako. Taonani lonjezo la Mulungu panopa pa Yesaya 9:6, 7.” Mungaŵerenge lembali m’Baibulo lanu kapena mawu ake osonyezedwa m’nkhaniyo mu Nsanja ya Olonda. Fotokozani mwachidule kuti Nsanja ya Olonda imachirikiza Ufumu wa Yehova monga chiyembekezo chokha cha dziko lamtendere, ndipo gaŵirani sabusikripishoni.

3 Pogaŵira “Galamukani!” wa November 8 munganene kuti:

◼ “Kodi muganiza bwanji za funsoli pachikuto cha magazini awa: ‘Nchifukwa Ninji Moyo Uli Waufupi Motere?’ [Yembekezani yankho.] Nkhani zimenezi zikufotokoza zimene asayansi amakono ndi ena anena pa ukalamba, ndiyeno zikufotokoza zimene Mlengi wathu walonjeza ponena za chiyembekezo cha moyo wosatha. Ndingakonde kukusiyirani kopeli pachopereka cha K100.00.”

4 Mukapeza anthu okonda zachipembedzo, bwanji osasonyeza nkhani ya mu “Nsanja ya Olonda” ya October 15? Ulaliki wotsatirawu ungadzutse chidwi:

◼ “Ndifuna kumva yankho lanu pa funsoli: Kodi nkotheka kukonda Mulungu ndi kumuwopa panthaŵi imodzimodzi?” Yembekezani yankho, ndiyeno ŵerengani lemba limene lazikidwapo nkhani yakuti “Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu Woona Tsopano?” (Mlal. 12:13) Gwiritsirani ntchito limodzi la mafanizo pamasamba 422-3 m’buku la Kukambitsirana, ndiyeno gaŵirani magaziniwo.

5 Pogwira ntchito kunyumba ndi nyumba, musalumphe masitolo aang’ono ndi mashopu. Aja amene amapita kumasitolo nthaŵi zonse amati ntchito imeneyi imakhala yosangalatsa ndi yobala zipatso. Mukhoza kuyesa ulaliki wosavuta wonga wotsatirawu pogaŵira “Galamukani!” wa October 8:

◼ “Tidziŵa kuti anthu amalonda amafuna kudziŵa zatsopano pankhani zokhudza dera lawo. Ndikhulupirira kuti nkhani zimenezi mudzakondwera nazo.” Ndiyeno auzeni mwachidule mfundo ina m’nkhani yakuti “Mabanja a Kholo Limodzi—Kodi Angapambane Kufika Pati?” Ndiyeno gaŵirani sabusikripishoni.

6 Ngati munthu amene mwafikira alidi wotanganitsidwa, mungasonyeze magazini ndi kuti:

◼ “Ndikudziŵa kuti simunali kuyembekezera mlendo lero, choncho sindidzakutayirani nthaŵi. Ndikufuna kukupatsani mwaŵi wa kuŵerenga kanthu kena kofunika kwambiri.” Sonyezani nkhani imene mwasankha, ndipo gaŵirani magaziniwo.

7 Sungani cholembapo cholongosoka cha kunyumba ndi nyumba, ndipo bwererani kwa onse amene munagaŵira magazini kukagaŵira sabusikripishoni ya magazini amodzi kapena onse aŵiri. Tiyeni tikhale okonzeka ndi atcheru kugaŵira magazini athu nthaŵi iliyonse yoyenera.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena