Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kunyamula kumka nazo ku misonkhano?
Mlungu uliwonse timalandira malangizo opindulitsa ndi chilimbikitso pamisonkhano ya mpingo. (Yes. 48:17; Aheb. 10:24, 25) Komabe, kuchuluka kwa mapindu amene timapeza kumadalira kwambiri pa kufikapo kwathu titakonzekera bwino kapena ayi.
Kungakhale bwino kwa wa m’banja aliyense kukhala ndi buku lakelake lophunziridwa ndi zinthu zina zofunikira pamisonkhano. Zimenezi zikuphatikizapo Baibulo, buku la nyimbo, chofalitsa (zofalitsa) chimene chikuphunziridwa, notibuku, ndi peni kapena pensulo.
Pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki, pafunikira Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki. Zinthu zimenezi zimatithandiza kukumbukira mitu ya nkhani za ophunzira zimene zikukambidwa ndi kutsatira woyang’anira sukulu pamene akupereka uphungu. Tingagwiritsire ntchito uphunguwo ndi malingaliro pa ife eni kuti tiwongolere nkhani zathu ndi maulaliki a utumiki wakumunda. Kuyambira m’January, nkhani zolangiza zazikidwa pa Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu kapena Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona. Kungakhale koyenera kwa wa m’banja aliyense kunyamula makope ake; kotero kuti akhale nawo kuti azikayang’anamo.
Pa Msonkhano Wautumiki, tifunikira kukhala ndi Utumiki Wathu Waufumu watsopano ndi buku la Kukambitsirana. Nyamulani zofalitsa zilizonse zimene zidzagwiritsiridwa ntchito pa msonkhanowo, monga ngati mabuku amene adzagwiritsiridwa ntchito m’zitsanzo za maulaliki. Akulu ayenera kukhala ndi kope la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu.
Makolo ayenera kuyesayesa kuchititsa ana awo kukhala chete ndi kumvetsera pamisonkhano ya mpingo. Kuwapatsa makope awo a Nsanja ya Olonda ndi zofalitsa zina, ngakhale asanadziŵebe kuŵerenga, kumawalimbikitsa kufuna kudziŵa. Pamene ana aphunzitsidwa kulemekeza zofalitsa zateokrase ndi kuzigwiritsira ntchito, amakhala ndi zizoloŵezi zauzimu zoyenera zamoyo wonse.
Chimwemwe ndi chikhutiro chimene timapeza m’misonkhano ya mpingo zimawonjezereka kwambiri pamene tifikapo tili okonzekera bwino lomwe. (2 Tim. 3:17) Imeneyi ndiyo njira yabwino koposa yotsimikizirira kuti tili ‘odzazidwa ndi chizindikiritso cha chifuniro [cha Mulungu] mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu.’—Akol. 1:9.