Kodi Muli ndi Gawo Lanulanu?
1. Kodi gawo lanulanu limakhala lotani?
1 Gawo lanulanu ndi limene lapatsidwa kwa inuyo. Likhoza kukhala pafupi poti mutha kumafikako msanga n’kumalalikira mwina nokha kapena ndi wofalitsa wina. Ngakhale kuti ndi bwino kuchirikiza zimene mpingo umakonza zoti anthu akalalikire monga gulu, kukhala ndi gawo lanulanu loti muzikalalikirako nthawi zina kungakuthandizeni kulalikira mokwanira, makamaka m’mipingo imene ili ndi gawo lalikulu.—Mac. 10:42.
2. Kodi ubwino wokhala ndi gawo lanulanu ndi wotani?
2 Ubwino Wake: Ena apeza ubwino wina wolalikira m’gawo lawolawo lapafupi ndi kuntchito kwawo panthawi yopuma masana kapena akangoweruka kuntchito. Ena amakonda kulalikirira limodzi monga banja m’dera lawo kwa ola limodzi kapena kuposerapo asanapite ku Phunziro la Buku la Mpingo. Chifukwa chochita zimenezi, maulendo obwereza ndi maphunziro a Baibulo amene anapeza anali apafupi, zomwe zinachepetsa mphamvu, nthawi, ndi ndalama zomwe anawononga. Popeza mukhoza kuchita zambiri mu nthawi yochepa, kukhala ndi gawo lanulanu kukhoza kuthandiza ena kuchita upainiya wothandiza nthawi ndi nthawi ngakhalenso kulembetsa kukhala apainiya okhazikika. Komanso, kukhala ndi gawo lathulathu n’kudziwana bwino ndi eninyumba kungatithandize kuti azitikhulupirira ndiponso tizinena zinthu zogwirizana ndi nkhawa zimene ali nazo. Zimenezi zingathandize kuti utumiki wathu ukhale wopindulitsa kwambiri.
3. Kodi n’chiyani chinachitikira mpainiya wina amene anapeza gawo lakelake?
3 Mpainiya wina amene analimbikitsidwa ndi woyang’anira dera kuti apeze gawo lakelake anati: “Ndinamvera malangizo amenewa ndipo posakhalitsa ndinadziwana bwino ndi eninyumba a m’gawo langa. Ndinasintha nthawi imene ndimapitako kuti igwirizane ndi nthawi imene amapeza mpata. Chifukwa cha zimenezi, maulendo anga obwereza anakwera kuchoka pa 35 kufika pa oposa 80 pamwezi, ndipo ndili ndi maphunziro a Baibulo 7.”
4. Kodi mungapeze bwanji gawo lanulanu ndipo mungalalikire bwanji m’gawo limeneli?
4 Mmene Mungalipezere: Ngati mukufuna kupempha gawo lanulanu, lankhulani ndi mtumiki wa magawo. Khalani omasuka kuuza wofalitsa wina kuti agwirire nanu limodzi ntchito, ndipo muzilemba nyumba zimene simunapezepo anthu. Muziyesetsa kumaliza gawolo m’miyezi inayi. Ngati zikukuvutani kuchita zimenezi, mungapemphe woyang’anira Phunziro la Buku la Mpingo kapena anthu ena kuti akuthandizeni. Pamapeto pa miyezi inayi, mukhoza kubweza gawo limene mwalimalizalo kapena mungapemphe kuti mulitengenso. Komabe, musamangosunga gawo lomwelomwelo mpaka kalekale koma muzilibweza kuti ena athe kulitenga. Ngati muli mu mpingo umene uli ndi gawo lochepa ndipo n’zosatheka kuti mukhale ndi gawo lanulanu, mwina mungapemphe kambali kochepa ka gawo kwa woyang’anira phunziro la buku lanu.
5. Kodi n’chiyani chikufunika kuti tikwaniritse ntchito yathu yolalikira?
5 Ntchito yathu yoti tilalikire “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu” ndi yaikulu kwambiri. (Mat. 24:14) Imafuna kuigwirira pamodzi mwadongosolo. Kulalikira gawo lathulathu powonjezera pa kulalikira monga gulu kungatithandize kufikira anthu ambiri omwe tingathe ndi uthenga wabwino.