Afikireni a Muukwati Amene Si Mboni
1 Zimakhala zosangalatsa kwenikweni ngati mwamuna ndi mkazi ali ogwirizana pakulambira koona. Komabe, m’mabanja ambiri, mmodzi yekha wa okwatiranawo ndiye amatenga njira ya choonadi. Kodi tingawafikire motani a muukwati amene si Mboni ndi kuwalimbikitsa kulambira Yehova limodzi nafe?—1 Tim. 2:1-4.
2 Dziŵani Bwino Maganizo Awo: Ngakhale kuti amuna kapena akazi osakhala Mboni amatsutsa, nthaŵi zambiri vuto lawo limakhala mphwayi kapena kusazindikira. Munthu amaona ngati akunyalanyazidwa kapena amachita nsanje ndi chipembedzo chatsopano cha mwamuna wake kapena mkazi wake. Mwamuna wina anati: “Nditatsala ndekha m’nyumba, ndinamva ngati wonyanyalidwa.” Winanso anati: “Ndinamva ngati mkazi wanga ndi ana anga akundisiya.” Amuna ena angaone ngati chipembedzo chikuwalanda banja lawo. (Onani Nsanja ya Olonda ya August 15, 1990, masamba 20-3.) Nchifukwa chake zimakhala bwino kwambiri kuti ngati nkotheka, tizipemphanso mwamuna kumakhala ndi mkazi wake paphunziro la Baibulo lapanyumba, kungoyambira pachiyambi.
3 Gwirani Ntchito Monga Kagulu: Mboni zina, mwamuna ndi mkazi wake, anagwira ntchito yamphamvu pothandiza mwamuna wina ndi mkazi wake kubwera m’choonadi. Mlongoyo atayamba phunziro ndi mkaziyo, mbaleyo anali kumachezera mwamunayo. Nthaŵi zambiri anali kutha kuyamba phunziro ndi mwamuna.
4 Khalani Waubwenzi ndi Wochereza: Mabanja ena mumpingo angathandize mwa kumacheza ndi mabanja ena amene sanagwirizanebe pakulambira koona. Maulendo angapo okawachezera mwaubwenzi angathandize mwamuna kapena mkazi wosakhala Mboni kuona kuti Mboni za Yehova ndi Akristu aulemu ndi ochitirana chifundo.
5 Nthaŵi ndi nthaŵi, akulu angamapende kuti aone kuti nzoyesayesa zotani zimene ena achita pofuna kuthandiza amuna kapena akazi osakhala Mboni ndiponso kuona kuti nchiyaninso chingachitidwe ndi chiyembekezo chowakopera kwa Yehova.—1 Pet. 3:1.