Kagwiritsireni Bwino Ntchito
1. Kodi kapepala kakuti Kudziwa Choonadi ndi kothandiza motani?
1 Kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? kanakonzedwa kuti kazitithandiza kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Komanso tingakagwiritse ntchito pomwaza mbewu za choonadi. (Mlal. 11:6) Ndime zotsatirazi zili ndi njira zina zimene zingatithandize kugwiritsa bwino ntchito kapepalaka.
2. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji kapepalaka kuti muyambe kukambirana ndi munthu?
2 Kuti Muyambe Kukambirana ndi Munthu: Mungamupatse mwininyumba kapepalako, n’kumuonetsa mafunso 6 amene ali pachikuto ndiyeno mungamufunse kuti: “Ndi funso liti limene inuyo munayamba mwadzifunsapo?” Akayankha, mungamusonyeze ndi kukambirana naye mayankho a m’Baibulo a funso limodzi limene wasankha. Kenako werengani lemba limodzi limene alisonyeza pakapepalaka. Pomaliza werengani kapena kufotokoza mwachidule tsamba lomaliza kenako mugawireni buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ngakhale mwininyumbayo atakana bukulo, walandira kale kapepala kaja, ndipo kakhoza kumuthandiza kuti mbewu za choonadi zimere mumtima mwake.—Mat. 13:23.
3. Kodi tingatani ngati tapeza mwininyumba ali wotanganidwa?
3 Ngati Mwininyumba Ali Wotanganidwa: Munganene kuti: “Popeza kuti ndakupezani nthawi yolakwika, ndingokusiyirani kapepala aka. Kali ndi mafunso 6 amene anthu ambiri amafunsa ndipo kakusonyeza momveka bwino zimene Baibulo limanena poyankha mafunso amenewo. Ndikadzabweranso, ndingakonde kudzamva maganizo anu.”
4. Kodi tingagawire bwanji kapepalaka tikamalalikira mumsewu?
4 Tikamalalikira Mumsewu: Munganene kuti: “Muli bwanji? Kodi munayamba mwafunsapo lililonse pa mafunso awa? [Yembekezani ayankhe.] Kapepalaka kakufotokoza mayankho omveka bwino ochokera m’Baibulo a mafunso amenewa.” Ngati munthuyo sakufulumira, mungakambirane naye yankho limodzi kuchokera pakapepalaka, mwinanso mungamugawire buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.
5. Kodi nthawi zina tingagwiritse ntchito bwanji kapepalaka tikapanda kupeza anthu pakhomo?
5 Ngati Sitinapeze Anthu Pakhomo: M’madera ena, ofalitsa akapanda kupeza anthu pakhomo, amasiya mabuku kapena magazini pamalo ena pakhomopo. Ngati mumachita zimenezi mumpingo wanu, mungachite bwino nthawi zina kusiya kapepala kakuti Kudziwa Choonadi. Ndiye mukadzafikanso munganene kuti: “Tsiku lina tinabwera koma sitinapeze aliyense, ndiye tinangokusiyirani kapepala aka. Kodi ndi mafunso ati pa mafunso awa amene mungakonde mutadziwa mayankho ake?”
6. N’chifukwa chiyani kapepala kakuti Kudziwa Choonadi kali kothandiza polalikira?
6 Kapepala kakuti Kudziwa Choonadi kamafotokoza choonadi mosavuta komanso mosapita m’mbali. Kamathandiza anthu achipembedzo komanso chikhalidwe chilichonse. Kapepalaka n’kosavuta kugawira, moti ana komanso ofalitsa atsopano akhoza kugawira. Kodi inuyo mumakagwiritsa ntchito paliponse pamene kakufunikira?