Zitsanzo za Ulaliki
Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo?
Apatseni kapepalako kuti aone mutu wake kenako n’kuwauza kuti: “Tikugwira ntchito imene ikuchitika padziko lonse youza anthu za uthenga umene uli pakapepalaka. Choncho tikukupemphani kuti mukawerenge kuti mudziwe zambiri.”
Ngati mukusiya kapepalaka panyumba imene palibe anthu, onetsetsani kuti mwakasiya pamalo osaonekera ndipo mukapinde bwinobwino.
Ngati munthu wasonyeza kuti akufuna kudziwa zambiri, mukhoza kumufunsa maganizo ake pa mayankho atatu omwe ali patsamba loyamba la kapepalaka. Muonetseni zimene lemba la Salimo 119:144, 160 lomwe lili mkati mwa kapepalako limanena. Kenako muuzeni kuti kapepalako kakunena za webusaiti yomwe ingamuthandize kupeza mayankho olondola m’Baibulo. Mwina mungam’sonyeze chitsanzo cha zimene zili pa webusaiti yathu pomusonyeza vidiyo yamutu wakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? Musanachoke, muonetseni mafunso atatu amene ali kumapeto kwa kapepalako ndipo muuzeni kuti atchule funso limene akufuna kudziwa yankho lake. Muuzeni kuti mudzabweranso kuti mudzakambirane yankho la m’Baibulo la funsolo pogwiritsa ntchito webusaiti yathu ya jw.org. Mukadzapitakonso, dzakambiraneni yankho la funsolo popita pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO.
Ngati pa nthawiyi mukugawiranso kapepala koitanira anthu kumsonkhano wachigawo, m’patseni munthuyo timapepala tiwiri tonseti n’kunena kuti: “Ndakupatsaninso kapepala kokuitanirani ku msonkhano wofunika kwambiri.”
Nsanja ya Olonda August 1
Kumapeto kwa mlungu, ngati mukuona kuti n’zoyenera kugawiranso Nsanja ya Olonda, munganene kuti: “Tilinso ndi magazini yatsopano iyi. Magaziniyi ikuthandizani kupeza yankho la funso lakuti, Kodi Mulungu amakuonani kuti ndinu wofunika?”
Galamukani! August
Kumapeto kwa mlungu, ngati mukuona kuti n’zoyenera kugawiranso Galamukani!, munganene kuti: “Tilinso ndi magazini yatsopano iyi. Magaziniyi ikuthandizani kupeza yankho la funso lakuti, Kodi mungatani kuti mugwirizanenso ngati mwayambana?”