Zitsanzo za Ulaliki
Nsanja ya Olonda April 1
“Tikugawira kapepala aka kwa aliyense m’dera lino. [Apatseni kapepala kakuti, Kodi Baibulo Mumalikhulupirira? Afunseni funso limene lili patsamba loyamba kuti anene maganizo awo pa mayankho atatu omwe ali pakapepalako. Aonetseni yankho la m’Baibulo la funsoli lomwe lili pa 2 Timoteyo 3:16, ndipo alimbikitseni kuti awerenge kapepalaka akapeza nthawi.] Anthu ambiri sadziwa kuti m’Baibulo muli mayankho ogwira mtima a mafunso awa. [Aonetseni mafunso omwe ali m’nkhani yoyamba mu Nsanja ya Olonda ya April 1.] Magaziniyi ikufotokoza mmene mungapezere mayankho a mafunsowa m’Baibulo.”
Galamukani! April
“Tikucheza ndi anthu mwachidule m’dera lino. Masiku ano anthu ambiri ali ndi nkhawa pa nkhani yolera ana. Poyamba makolo ndi amene amauza ana zochita. Koma masiku ano, m’mabanja ambiri ana ndi omwe akumauza makolo zochita. Kodi makolo akulangiza ana ngati mmene ziyenera kukhalira? [Yembekezerani ayankhe.] Baibulo limati kulangiza ana komanso kuwapatsa chilango akalakwitsa n’kofunika kwambiri. [Werengani Miyambo 29:17.] Magaziniyi ikufotokoza malangizo a m’Baibulo omwe angathandize makolo kulera bwino ana awo.”