Tili ndi Chida Chatsopano Choyambitsira Maphunziro!
1 Mayi wina wa ku America anali Mkatolika wodzipereka. Ankasunga mokhulupirika ziphunzitso za tchalitchichi mpakana anapita paulendo wachipembedzo ku Vatican. Komano, Mboni za Yehova zitam’peza panyumba yake, anavomera kuti aziphunzira nazo Baibulo. N’chifukwa chiyani anavomera? Ankafuna kuphunzira zimene Baibulo limanena koma tchalitchi chake sichinali kuphunzitsa Baibulo panyumba. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Zikutiphunzitsa kuti sitingadziŵe amene angavomere phunziro la Baibulo laulere.—Mlal. 11:6.
2 Kodi munagwapo ulesi kuuza anthu kuti timafunitsitsa kuphunzira Baibulo ndi aliyense amene akufuna? Kodi aliyense m’dera lanu akudziŵa kuti timaphunzitsa zimenezi kwaulere? Kodi tingadziŵe bwanji kuti amadziŵa zimenezi? Mwa kugwiritsa ntchito chida chatsopano! Ndi thirakiti lokongola la masamba asanu ndi limodzi la mutu wakuti Kodi Mukufuna Kudziŵa Zambiri za Baibulo? Tiyeni tilidziŵe bwino thirakitili. Tipenda kamutu kalikonse pakokha.
3 “N’chifukwa Chiyani Muyenera Kuŵerenga Baibulo?” Zifukwa zimene thirakitili likunena n’zosangalatsa kwambiri. Likufotokoza kuti Baibulo lili ndi “malangizo achikondi ochokera kwa Mulungu,” a mmene tingam’pemphere thandizo m’pemphero ndiponso mmene tingalandirire mphatso yake ya moyo wosatha. (1 Ates. 2:13) Thirakiti limeneli lili ndi “choonadi [chosiyanasiyana cha m’Baibulo] chimene chimaunikira,” monga zomwe zimachitika tikamwalira ndi chifukwa chake padziko pano pali mavuto ambiri. Limafotokoza “mfundo zachikhalidwe za Mulungu zimene zili m’Baibulo” kuti tikagwiritsa ntchito mfundozi tidzapindula mwakuthupi ndipo tidzapeza chimwemwe, chiyembekezo, ndi makhalidwe ena abwino kwambiri. Thirakitili limatchulanso chifukwa china choŵerengera Baibulo—kuti tidziŵe maulosi a m’tsogolo osonyeza zimene zichitike patsogolo pathu pomwepa.—Chiv. 21:3, 4.
4 “Thandizo Kuti Timvetse Baibulo”: Thirakiti limeneli likuti: “Tonsefe timafuna thandizo kuti timvetse Mawu a Mulungu.” Ndiyeno limafotokoza njira yathu yophunzirira Baibulo: “Kaŵirikaŵiri zimakhala bwino kwambiri kuphunzira Baibulo pang’onopang’ono, kuyamba ndi ziphunzitso zoyambirira.” Komanso thirakitili likunena mwatchutchutchu kuti “Baibulo ndiye gwero lake,” ndipo mosabisa mawu limati bulosha lakuti Mulungu Amafunanji ndi limene lidzathandize wophunzira “kumvetsa Malemba amene amafotokoza nkhani zosiyanasiyana.” Kamutu kotsatira kali ndi funso losangalatsa kwambiri.
5 “Kodi Ndinu Wokonzeka Kupatula Nthaŵi Mlungu Uliwonse Kuti Mumvetse Baibulo?” Thirakitili likufotokoza kuti phunziro la Baibulo lingakonzedwe kuti lizichitika pamalo ndi nthaŵi imene wophunzirayo akufuna, kaya kunyumba kwake kapena patelefoni. Kodi n’ndani amene angakhale nawo pa phunziroli? Thirakitili likuti: “Banja lanu lonse. Mungauzenso anzanu ena onse kuti adzakhale nawo pa phunziroli. Ngati mukufuna, akhoza kumaphunzira ndi inu nokha basi.” Kodi munthu angaphunzire kwa nthaŵi yaitali motani? Likuti: “Ambiri amapatula ola limodzi pamlungu kuti aphunzire Baibulo. Kaya mungathe kupatula nthaŵi yambiri yoposa pamenepa kapena ayi, kapena mumakhala ndi nthaŵi yochepa, Mboni zidzakuthandizani.” Imeneyi ndiye mfundo yofunika! Ndife ofunitsitsa kusintha zinthu kuti tigwirizane ndi mmene wophunzira aliyense alili.
6 “Pempho Lakuti Muphunzire”: Pali kadanga komwe munthu amene walandira thilakitili angafunsirepo bulosha lakuti Mulungu Amafunanji kapena kupempha kuti munthu afike kudzamuuza zochuluka za pulogalamu yathu ya phunziro la Baibulo lapanyumba laulere. Asonyezaponso momwe chikuto cha bulosha limeneli chimaonekera. Kodi mukuona chifukwa chake thirakiti limeneli lidzalimbikitsire anthu oona mtima ambiri kuvomera kuti tiwathandize? Tsopano, kodi tingagwiritse ntchito motani chida chatsopano chimenechi?
7 Kodi Mupatse Ndani Mathirakiti Ameneŵa? Mathirakitiŵa mungapatse anthu pamaso m’pamaso kapena mungasiye panyumba yomwe simunapeze anthu. Tingagaŵire kunyumba ndi nyumba, munsewu, ndi m’gawo la anthu amalonda. Agaŵireni anthu kaya alandira mabuku athu kapena akana. Liikeni m’magazini kapena mabuku amene mukugaŵira. Litumizeni pamodzi ndi makalata amene mwalembera anzanu. Auzeni amene mumalankhulana nawo patelefoni kuti muwatumizira thirakiti. Khalani ndi mathirakitiŵa nthaŵi zonse kuti mugaŵire pokagula zinthu, kaya mwakwera zoyendera za anthu onse, ndiponso polalikira mwamwayi. Anthu onse obwera kunyumba kwanu apatseni thirakiti. Apatseni achibale anu, anansi, anzanu a kuntchito, anzanu a kusukulu, ndi odziŵana nawo ena. Yesetsani kuwapatsa anthu onse amene mwakumana nawo thirakiti limeneli! Zikatero titani?
8 Ngati Ayankhiratu: Anthu ena adzayankhiratu kuti akufuna kuphunzira Baibulo. Choncho, nthaŵi zonse popita mu utumiki wakumunda, onetsetsani kuti mwatenga mabulosha aŵiri a Mulungu Amafunanji—limodzi la wophunzira wanu, linalo lanu. Ngati munthuyo akufuna, yambani kuphunzira nthaŵi yomweyo. Tsegulani m’kati mwa chikuto, ndipo ŵerengani pamene pali mawu akuti “Mmene Mungagwiritsire Ntchito Bulosha Lino.” Ndiyeno pitani pa phunziro 1, ndipo m’sonyezeni mmene muzichitira. Kodi n’zovuta zimenezi?
9 Ngati Munthuyo Akufuna Kuti Aganize Kaye: Bwereraniko mofulumira. Popita onani kuti mwatenga bulosha lakuti Mulungu Amafunanji. Muonetseni zam’katimo zimene zili pa tsamba 2. M’siyeni asankhe phunziro limene akuliona kuti n’losangalatsa kwambiri. Pitani paphunzirolo, ndiyeno yambani kukambirana phunziro wasankhalo.
10 Pitani kwa Anthu Amene Analandira Magazini: Ngati munam’siyira wina thirakiti ndi magazini ena, mungayambe motere: “Nditabwera nthaŵi ija, ndinasangalala kukusiyirani magazini ya Nsanja ya Olonda. Mwina munaona kuti mutu wonse wa magazini imeneyi ndi Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Lero ndikufuna kufotokoza tanthauzo la Ufumu umenewu ndi zimene udzakuchitireni pamodzi ndi banja lanu.” Ndiyeno tsegulani bulosha la Mulungu Amafunanji pa phunziro 6. Yambani ndime yoyamba, kuŵerenga ndi kukambirana malinga ndi nthaŵi imene mwininyumbayo ali nayo. Ndiyeno konzani zoti mudzam’pezenso tsiku lina kudzamaliza phunzirolo.
11 Musakhale Opanda Mathirakiti: Nthaŵi zonse pampingo, woyang’anira utumiki ndi abale amene amasamalira mabuku adzafunika kuonetsetsa kuti ali ndi mathirakiti okwanira a Kudziŵa Baibulo. Sungani ena m’thumba lanu kapena m’chikwama chanu cha m’manja, m’galimoto yanu, pamalo anu antchito, kusukulu, pafupi ndi khomo loloŵera m’nyumba yanu—paliponse pamene sangatalikire. Inde, tengani ena m’chikwama chanu cha ku ulaliki kuti mwina mungakumane ndi amene mungakambirane naye za Baibulo.
12 Yehova Adalitsetu Khama Lathu: Cholinga chabwino cha Akristu onse ndicho kuphunzitsa munthu wina choonadi. (Mat. 28:19, 20) Kodi panopo muli ndi phunziro la Baibulo lapanyumba? Ngati muli nalo, kodi pandandanda yanu ya mlungu ndi mlungu mungapeze nthaŵi yochititsira phunziro lina? Ngati panopo mulibe phunziro, mosakayikira mukulifuna. Pemphani Yehova kuti adalitse khama lanu kuti mupeze wina amene mungaphunzire naye. Ndiyeno zochita zanu zikhale zogwirizana ndi mapemphero anuwo.—1 Yoh. 5:14, 15.
13 Tili ndi chida chatsopano choyambitsira maphunziro! Lidziŵeni bwino thirakitili. Agaŵireni mosaumira. Chitani zonse zimene mungathe kuti ‘muchite zabwino, ochuluka mu ntchito zabwino, owoloŵa manja, okonzeka kugaŵira ena’ zimene mwaphunzira m’Mawu a Mulungu.—1 Tim. 6:18, NW.
[Bokosi patsamba 4]
POFUNIKA KUGAŴIRA MATHIRAKITI
◼ Pokambirana zinthu za masiku onse
◼ Akalandira magazini athu
◼ Nyumba imene sitinapeze anthu
◼ Paulendo wobwereza
◼ Amene takumana nawo mu ulaliki wa mumsewu
◼ Polalikira m’gawo la anthu amalonda
◼ Polalikira mwamwayi
◼ Polemba makalata
◼ Tikakwera zoyendera za anthu onse
◼ Anthu akabwera kunyumba kwathu
◼ Polankhula ndi achibale, anansi, anzathu a kuntchito, anzathu a kusukulu, ndi odziŵana nawo ena