Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira June 27, 2011. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa mkati mwa milungu ya May 2 mpaka June 27, 2011. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.
1. Kodi tingaphunzirepo phunziro lotani pamene Yehova anafuna kuti Yobu apempherere anthu amene anam’lakwira? (Yobu 42:8) [w98 8/15 tsa. 30 ndime 5]
2. Kodi “nsembe zachilungamo” zimene Akhristu amapereka masiku ano n’chiyani? (Sal. 4:5) [w06 5/15 tsa. 18 ndime 9]
3. Kodi impso za Davide zinamuwongolera motani? (Sal. 16:7) [w04 12/1 tsa. 14 ndime 9]
4. Kodi “zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu” motani? (Sal. 19:1) [w04 10/1 tsa. 10 ndime 8]
5. Kodi Salimo 27:14 limasonyeza bwanji kugwirizana kwa chiyembekezo ndi kulimba mtima? [w06 10/1 tsa. 26-27 ndime 3 ndi 6]
6. Kodi lemba la Salimo 37:21 liyenera kutikhudza bwanji pa zochita zathu ndi abale athu? [w88 8/15 tsa. 17 ndime 8]
7. Pa nkhani yoyamikira, kodi tingaphunzire chiyani kwa Mlevi wina amene anali kudziko la ukapolo? (Sal. 42:1-3) [w06 6/1 tsa. 9 ndime 3]
8. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tizikonda chilungamo n’kumadana ndi zoipa? (Sal. 45:7) [cf tsa. 58-59 ndime 8-10]
9. Kodi ndi “mzimu wofunitsitsa” wa ndani umene Davide anapempha kuti umuchirikize? (Sal. 51:12) [w06 6/1 tsa. 9 ndime 10]
10. Kodi tingatani kuti tikhale ngati mtengo wa maolivi m’nyumba ya Mulungu? (Sal. 52:8) [w00 5/15 tsa. 29 ndime 6]