Ndandanda ya Mlungu wa June 20
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 20
Nyimbo Na. 17 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 8 ndime 18-22 ndi bokosi patsamba 86 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 45–51 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 48:1– 49:9 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Ufumu wa Mulungu Ndi Boma Lenileni?—rs tsa. 375 ndime 1 ndi 2 (Mph. 5)
Na. 3: Popeza Kuti Moyo Ndi Mphatso, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukonza Chipulumutso Chathu?—Aroma 6:23; Afil. 2:12 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Mabuku Ogawira M’mwezi wa July. Nkhani yokambirana. Fotokozani mwachidule timabuku togawira mu July ndiponso zimene zili mmenemo. Kenako chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri za mmene tingagawirire timabukuto.
Mph. 10: M’kamwa Mwa Ana. (Werengani Mateyu 21:15, 16) Kambiranani ndi omvera zinthu zothandiza zimene onse mumpingo, makamaka makolo, angachite kuti athandize ana awo kukhala kumbali ya Yehova pamene ali achinyamata. Limbikitsani onse kuti azitsanzira zimene Yesu ankachita popatula nthawi yocheza ndi ana komanso kumva maganizo awo ndi zofuna zawo.
Mph. 10: “Ulaliki wa Mumsewu Wopindulitsa.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho, yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Kambani nkhaniyi mogwirizana ndi mmene zinthu zilili kwanuko. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo imodzi kapena ziwiri za m’nkhaniyi.
Nyimbo Na. 16 ndi Pemphero