Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 3/12 tsamba 2
  • Muzilalikira Molimba Mtima Kumalo a Ntchito ndi Amalonda

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzilalikira Molimba Mtima Kumalo a Ntchito ndi Amalonda
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kulalikira M’gawo Lamalonda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Mmene Tingalalikirire M’gawo la Malonda
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Lalikirani Uthenga Wabwino Paliponse
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukonzekera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 3/12 tsamba 2

Muzilalikira Molimba Mtima Kumalo a Ntchito ndi Amalonda

1. N’chifukwa chiyani sitiyenera kutaya mtima ngati timachita mantha tikaganizira zolalikira kumalo a ntchito ndi amalonda?

1 Kodi mumachita mantha mukaganizira zolalikira kumalo a ntchito ndi amalonda? Ngati zili choncho, musataye mtima chifukwa ngakhalenso Paulo amene anali munthu wolimba mtima ndiponso wopanda mantha anafunika ‘kulimba mtima’ kuti alalikire. (1 Ates. 2:2) M’munsimu tikambirana zinthu zimene anthu ambiri amada nazo nkhawa komanso mfundo zimene zingathandize kuthetsa nkhawa zimenezi.

2. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuda nkhawa ndi zoti tingakhumudwitse anthu ogwira ntchito?

2 Kodi Ndikakhumudwitsa Anthu Amene Akugwira Ntchito? Anthu ambiri amene amagwira ntchito amakhala akuthandiza munthu aliyense amene wabwera, choncho amayembekezera kudodometsedwa. Nthawi zambiri amachita zinthu mwaulemu chifukwa angakuoneni ngati mwabwera kudzagula malonda kapena kudzagwira ntchito. Mukamavala modzilemekeza, kukhala wansangala ndiponso womasuka ndiye kuti azikulandirani mwaulemu.

3. Kodi tingapewe bwanji kukhumudwitsa anthu ogula malonda?

3 Kodi Ndikalalikira Pamaso pa Anthu Ambiri Ogula Malonda? Ngati n’zotheka, muzisankha nthawi imene anthu sakhala otanganidwa kwambiri kumalo amalonda ngati nthawi imene akutsegula kumene. Dikirani kufikira nthawi imene bwana kapena woyang’anira antchito ali yekha kuti mumulalikire. Muzilalikira mwachidule kwambiri.

4. Kodi tinganene chiyani tikamalalikira m’gawo la malonda?

4 Kodi Ndinganene Chiyani? Ngati pali anthu angapo ogwira ntchito muzilankhula ndi bwana wawo. Munganene kuti: “Tabwera kuntchito kwanu kuno lero chifukwa chakuti anthu amene amagwira ntchito sapezeka pakhomo. Ndikudziwa kuti muli pa ntchito, choncho ndilankhula nanu mwachidule.” Kuti asatione ngati ogulitsa malonda, zingakhale bwino kuti tisamanene za zopereka pokhapokha ngati atatifunsa za mmene timapezera ndalama zoyendetsera ntchito yathu. Mungapemphe bwana wa pamalopo kuti mulankhule ndi ogwira ntchito malinga ndi ntchito imene amagwira. Bwerezani zimene mwalankhula ndi bwana wawo. Ngati wogwira ntchitoyo ndi wotanganidwa, mulankhule naye mwachidule ndipo mumusiyire kapepala. Ngati n’zosatheka kulankhula ndi ogwira ntchitowo, mwina mungasiye mabuku pamalo amene amachezera nthawi yopuma kapena pamalo ena.

5. Tchulani zifukwa zotichititsa kulalikira kumalo a ntchito ndi amalonda molimba mtima.

5 Yesu ndi Paulo ankalalikira kwa anthu pamalo awo ogwirira ntchito molimba mtima ndipo inunso mukhoza kuchita chimodzimodzi. (Mat. 4:18-21; 9:9; Mac. 17:17) Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhazika mtima pansi ndiponso kuti mulimbe mtima. (Mac. 4:29) Nthawi zambiri anthu amapezeka kumalo ogwirira ntchito ndi amalonda, choncho bwanji osayesako kulalikira kumalo amenewa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena