Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kulalikira M’gawo Lamalonda
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Popeza anthu ambiri amakhala masana onse ali kumalo amene amachitira malonda, njira yabwino yowapezera anthu amenewa ndi kupita kumalo a malonda komweko. Tikamalalikira m’gawo lamalonda, timapeza anthu ambiri oti n’kuwalalikira ndipo anthuwo amatilandira mwaulemu poganiza kuti tikufuna kuwagula malonda. Choncho kulalikira m’gawo lamalonda kukhoza kukhala kosangalatsa ndiponso kungakhale ndi zotsatira zabwino. Komabe kuti tilalikire bwino m’gawo lotereli, tiyenera kuchita zinthu mozindikira komanso tiyenera kuvala ndi kudzikongoletsa moyenera. (2 Akor. 6:3) Choncho woyang’anira utumiki ayenera kuonetsetsa kuti gawo lamalonda limapitidwa kawirikawiri komanso kuti ofalitsa amene amapita m’gawolo ndi oyenerera.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Pa kulambira kwanu kwa pabanja, konzekerani ndi kuyeserera zimene munganene mwachidule polalikira, ngati mutapemphedwa kuti mukalalikire m’gawo lamalonda.