Ndandanda ya Mlungu wa September 21
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 21
Nyimbo Na. 47 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 19 ndime 1-8 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 19-22 (8 min.)
Na. 1: 2 Mafumu 20:12-21 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Yehova Amapulumutsa Anthu Ake—dp tsa. 77-79 ndime 18-21 (5 min.)
Na. 3: Kodi Mawu Akuti “Amen” Amatanthauza Chiyani?—bh tsa. 170 ndime 15 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Muzichitira umboni mokwanira za uthenga wabwino.’—Mac. 20:24.
10 min: Kodi Tinachita Zotani Chaka cha Utumiki Chathachi? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani zimene mpingo wanu unachita m’chaka cha utumiki chathachi, makamaka zinthu zabwino zimene unakwanitsa kuchita, ndipo uyamikireni. Tchulani mfundo imodzi kapena ziwiri zimene mpingo wanu uyenera kukonza m’chaka chimene talowachi, ndipo fotokozani zimene mungachite kuti mukwanitse zimenezi.
10 min: Kuchitira Umboni Mokwanira Kumakhala ndi Zotsatira Zabwino. Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2015, tsamba 54 ndime 1, tsamba 56 ndime 2 mpaka tsamba 57 ndime 1. Komanso tsamba 63 ndime 2 mpaka tsamba 64 ndime 1. Mukamaliza kukambirana nkhani iliyonse, pemphani omvera kuti afotokoze zimene akuphunzirapo.
10 min: “Kodi Tingawalalikire Bwanji Achibale Athu Omwe si Mboni?” Nkhani yokambirana. Fotokozani zomwe tingachite kuti tithandize achibale athu kuphunzira choonadi.
Nyimbo Na. 81 ndi Pemphero