Ndandanda ya Mlungu wa September 14
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 14
Nyimbo Na. 114 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 18 ndime 20-24 ndi bokosi patsamba 188 (30 min.)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 16-18 (8 min.)
Na. 1: 2 Mafumu 17:12-18 (Osapitirira 3 min.)
Na. 2: Kodi Mungatani Kuti Muzipindula Kwambiri Mukamawerenga Baibulo?—igw tsa. 32 (5 min.)
Na. 3: Muzithandiza Atumiki a Yehova Mopanda Mantha—bt tsa. 135-136 ndime 11-14 (5 min.)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: ‘Muzichitira umboni mokwanira za uthenga wabwino.’—Mac. 20:24.
10 min: ‘Muzichitira Umboni Mokwanira Uthenga Wabwino.’ Nkhani yochokera pa mutu wa mwezi uno komanso m’buku lakuti, Kuchitira Umboni, mutu 1, ndime 1-11.—Mac. 20:24.
20 min: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kulalikira M’gawo Lamalonda.” Nkhani yokambirana. Chitani chitsanzo chachidule chokhala ndi mbali ziwiri. Mbali yoyamba isonyeze wofalitsa akulephera kuchita zinthu mozindikira pamene akulalikira kwa munthu wogulitsa malonda. Mbali yachiwiri isonyeze wofalitsayo akuchita zinthu mozindikira. Ndiyeno funsani omvera kuti afotokoze chifukwa chake akuona kuti m’chitsanzo chachiwirichi wofalitsayo wachita bwino.
Nyimbo Na. 96 ndi Pemphero