Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Kuwonjezera pa ofesi yomasulira mabuku m’Chitumbuka yomwe ili ku Mzuzu, tatsegulanso ofesi ina yomasulira mabuku m’Chitonga ku Chintheche, m’boma la Nkhatabay, komanso m’Chikyangonde, ku Karonga. Posachedwapa titsegulanso ofesi ina yomasulira mabuku m’Chiyao ku Namwera, m’boma la Mangochi. N’zodziwikiratu kuti izi zithandiza kuti anthu ambiri azimva uthenga wa m’Baibulo m’chilankhulo chawo.—Mac. 2:8, 11.