Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukonzekera
1 Kukonzekera bwino utumiki kumatithandiza kuti tisonyeze ena chidwi. Chifukwa chiyani? Ngati takonzekera bwino sitimaganizira kwambiri zimene tikufuna kunena koma m’malo mwake chidwi chathu chonse chimakhala pa mwininyumba. Ndiponso zimatithandiza kuti tisakhale ndi mantha polankhula ndipo timalankhula motsimikiza mtima. Komabe, kodi tingakonzekere bwanji ulaliki wogwira mtima?
2 Gwiritsani Ntchito Ulaliki Woyenera: Pa maulaliki a mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2006, sankhani ulaliki umodzi woyenererana ndi kwanuko, ndipo ganizirani momwe mungaufotokozere m’mawu anuanu. Usintheni kuti uyenererane ndi gawo lanu. Mwachitsanzo, ngati kugawo lanu kuli anthu achipembedzo china chake kapena anthu a mtundu wina wake, ganizirani zimene munganene kuti ulaliki wanu ukhale wogwira mtima. Kusintha ulaliki wanu kuti uyenererane ndi anthu amene mumalankhula nawo kumasonyeza kuti muli nawo chidwi anthuwo.—1 Akor. 9:22.
3 Pamene mukugwiritsa ntchito ulalikiwo pitirizanibe kumausintha. Popeza kuti mawu oyamba amakhala ofunika kwambiri, onani mmene anthu akuchitira mukangoyamba kulankhula. Kodi akusangalala ndi nkhani imene mukuwauza? Kodi akukuyankhani mafunso amene mukufunsa? Ngati si choncho, sinthani ulaliki wanu mpaka mutapeza ulaliki umene ungakhale wogwira mtima kwambiri.
4 Zothandiza Kukumbukira: Ambiri zimawavuta kukumbukirabe ulaliki pamene afika pakhomo la munthu. Ngati ndi choncho, kodi mwayesererapo ulaliki wanu ndi wina wake? Zimenezi zingakuthandizeni kuti musaiwale mfundo zofunikira ndi kuti mukazikambe mosavuta ndi motsatirika bwino. Izi zingakuthandizeninso kudziwa mmene mungachitire anthu atakuyankhani mosiyanasiyana.
5 Chinanso chimene chingakuthandizeni kukumbukira ndicho kulemba mfundo zofunika kwambiri pa kapepala ndi kuziwerenga pamene mukuyandikira pa nyumba. Ena amaona kuti kapepala kameneka kamawathandiza kuti asakhale ndi mantha koma kuti athe kulankhula bwino. Choncho, kukonzekera bwino kungatithandize kusonyeza ena chidwi ndi kulalikira uthenga wabwino mogwira mtima.