Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukhala Wokhoza Kusintha
1 Mtumwi Paulo anasonyeza chitsanzo chabwino posintha ulaliki wake kuti ugwirizane ndi maganizo ndi nzeru za anthu amene amawalalikira za uthenga wabwino nthawi zonse. (1 Akor. 9:19-23) Tiyenera kuyesayesa kuchita chimodzimodzi. Mwa kuganizira kaye, tingathe kusintha zitsanzo za maulaliki zimene zimakhala mu Utumiki Wathu wa Ufumu kuti zigwirizane ndi zosowa za anthu a m’gawo lathu. Tikafika pa khomo, tingathe kuona zinthu zimene mwini nyumba amakonda n’kuziphatikiza mu ulaliki wathu. Komabe, pali njira inanso imene tingasinthire ulaliki wathu.
2 Kusintha Ulaliki Wathu Mogwirizana N’zimene Eni Nyumba Akunena: Polalikira uthenga wabwino, kawirikawiri timafunsa funso ndipo timayembekeza kuti eni nyumba ayankhe. Kodi mumawaona bwanji mayankho amene iwo amapereka? Kodi timakonda kungowayamikira basi kenaka n’kupitiriza kulankhula zomwe tinakonzekera? Kapena kodi zimene mumalankhula zimasonyeza kuti mukuganizira za mayankho amene eni nyumbawo apereka? Ngati mumasonyeza chidwi chenicheni ndi zimene ena amanena, mungafunse mwanzeru mafunso owonjezera kuti mudziwe zimene iwo akuganiza. (Miy. 20:5) Choncho mungalalikire za uthenga wa Ufumu umene ukukhudzana mwachindunji ndi nkhawa za omvera anu.
3 Zimenezi zimafuna kuti tizikhala okonzeka kulankhula za nkhani zina zimene sitinakonzekere kuti tikakambe. Ngati titayamba kulankhula za nkhani ina imene tinaimva pa wailesi ndipo mwini nyumba watchula za nkhani imene yachitika kwawoko kapena nkhani imene yam’khudza, chidwi chathu chofuna kukwanitsa zosowa za mwini nyumba chidzatipangitsa kusintha ulaliki wathu n’kuyamba nkhani imene ikumukhudza kwambiri mwini nyumbayo pogwiritsa ntchito Baibulo.—Afil. 2:4.
4 Kusintha Kachitidwe Kathu: Ngati mwini nyumba wafunsa funso, zingatithandize ngati tingapitirize kukambirana naye za nkhaniyo nthawi ina pamene tapeza mfundo zina pa nkhani imeneyo. Tingamupatsenso mabuku amene akulongosola bwino za nkhani imeneyo. Zonsezi zimaonetsa kuti tikusonyeza chidwi chenicheni chothandiza ena kuti am’dziwe Yehova.—2 Akor. 2:17.