Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzisonyeza Chidwi Munthu Amene Mukumulalikira
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Yesu ankakonda komanso kusonyeza chidwi munthu aliyense. Mwachitsanzo, pa nthawi ina anazindikira kuti munthu wina wosamva ankachita manyazi. Choncho, anamutengera pambali n’kukamuchiritsa. (Maliko 7:31-35) Komanso anasonyeza kuti ankaganizira ophunzira ake. Sankawaphunzitsa zinthu zambirimbiri nthawi imodzi, chifukwa ankadziwa kuti sangathe kumvetsa zonse. (Yoh. 16:12) Atapita kumwamba, ankasonyezabe kuti amakonda anthu ndiponso kuwaganizira. (2 Tim. 4:17) Popeza ndife otsatira ake, tiyenera kumutsanzira. (1 Pet. 2:21; 1 Yoh. 3:16, 18) Ndipotu munthu angamvetsere uthenga wathu ngati ataona kuti tili naye chidwi, tikumuganizira komanso tikuyesetsa kumvetsa mavuto ake. Zikatere amadziwa kuti cholinga chathu sikungomuuza uthenga womwe tabweretsa kapena kumupatsa mabuku athu, koma tikufunitsitsa kumuthandiza.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Pa kulambira kwa pabanja, konzekerani mmene mungasinthire ulaliki wanu kuti ugwirizane ndi zimene munthu wanena. Kapena mungachite zimenezi pamene mukuchoka nyumba ina kupita nyumba ina.
Pa nthawi ya msonkhano wokonzekera utumiki, m’bale amene akuchititsa msonkhanowu afotokoze, kapena akonze zoti pakhale chitsanzo choonetsa zimene tingachite posonyeza chidwi munthu amene tikumulalikira.