Sonyezani Ena Chidwi mwa Kuyang’anitsitsa Zinthu
1 Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu ali ndi luso lozindikira zosowa zenizeni za anthu ndi kuwapatsa thandizo loyenerera. (2 Mbiri 16:9; Marko 6:34) Kuzindikira zinthu zimene anthu amene timakumana nawo mu utumiki amazikonda ndi zimene amada nazo nkhawa, kungatithandize kuti tisinthe ulaliki wathu wa uthenga wabwino kuti ugwirizane ndi zosowa komanso zokonda za anthuwo.
2 Khalani Tcheru: Yesu ankayang’anitsitsa zinthu. (Marko 12:41-43; Luka 19:1-6) Mofanana ndi Yesu, pamene tafika pa khomo la munthu tizikhala ndi chidwi choona zinthu ngati zokongoletsa za chipembedzo, mawu olembedwa pa magalimoto, kapena zoseweretsa ana. Zimenezi zingatithandize kuti tilalikire uthenga wabwino mogwira mtima.
3 Nkhope ya munthu ndi zochita zake zingatithandize kuzindikira zimene zili mumtima mwake. (Miy. 15:13) Mwina imfa ya wokondedwa wake kapena vuto linalake limene lamugwera, zingamupangitse kufuna chitonthozo. Angayamikire kwambiri ngati mutamupatsa malemba oyenererana ndi vuto lakelo. (Miy. 16:24) Kodi mwininyumba akuoneka kuti akufulumira kuti achoke kapena akutonthoza mwana? Ngati zili choncho, mungachite bwino kukonza zobwera nthawi ina. Chifukwa choganizira ena mwa njira imeneyi ndi kukhala “ochitirana chifundo,” ena angatimvetsere pamene tabwererako.—1 Pet. 3:8.
4 Sinthani Ndemanga Zanu: Mtumwi Paulo anaona kuti mzinda wa Atene unali ndi guwa la nsembe loperekedwa “Kwa Mulungu Wosadziwika.” Poona zimenezi, iye anasintha ulaliki wake, pakuti anati: “Chimene muchipembedza osachidziwa, chimenecho ndichilalikira kwa inu.” Chifukwa cha luso limene Paulo analisonyeza pofikira anthuwo, ena amene analipo anamvetsera uthenga wa Ufumu ndipo anakhala okhulupirira.—Mac. 17:23, 34.
5 Mofanana ndi zimenezi, kuyang’anitsitsa kwathu zinthu kutithandize kuzindikira zimene anthu amakonda ndiyeno kusintha ulaliki wathu kuti ugwirizane ndi zimenezo. Funsani mafunso amene adzalimbikitsa mwininyumba kukuuzani maganizo ake. Ganizirani za malemba amene angagwiritsidwe ntchito kukulitsa chidwi chake. (Miy. 20:5) Tikakhala oyang’anitsitsa zinthu ndi kusonyeza ena chidwi chenicheni, tidzatha kulalikira uthenga wabwino mwaluso.