Ndandanda ya Mlungu wa November 17
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 17
Nyimbo Na. 113 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 4 ndime 10-18 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 23-27 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 25:17-19 ndi 26:1-10 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani ya Moyo—rs tsa. 295 ndime 1-5 (Mph. 5)
Na. 3: Njira Yokhayo Yoyenera Kugwiritsa Ntchito Magazi—bh tsa. 131-133 ndime 17-19 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Kodi Ndiyenera Kubatizidwa? Nkhani yokambirana yochokera m’buku lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri tsamba 304 mpaka 307. Kambiranani mafunso otsatirawa: (1) Kodi ubatizo umaimira chiyani? (2) Kodi kudzipereka kwa Yehova kumatanthauza chiyani? (3) Kodi muyenera kumachita zotani musanabatizidwe? (4) Kodi munthu ayenera kubatizidwa akafika zaka zingati? (5) Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mukufuna kubatizidwa koma makolo anu akukuuzani kuti mudikireTimadziwika Chifukwa cha Chikondi. (Yoh. 13:35) kaye?
Mph. 10: Nkhani yokambirana yochokera mu Buku Lapachaka la 2014, tsamba 48 ndime 1 mpaka tsamba 49 ndime 3. Komanso tsamba 69 ndime 1 mpaka tsamba 70 ndime 2. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene tikuphunzirapo.
Mph. 10: “Njira Yosangalatsa Yolalikirira M’malo Opezeka Anthu Ambiri.” Mafunso ndi mayankho. Ngati mpingo wanu uli ndi malo omwe amapezeka anthu ambiri, funsani woyang’anira utumiki kuti anene zimene mpingo wakonza za njira imeneyi. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene zinachitika pamene ankagwiritsa ntchito njirayi.
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero