Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/08 tsamba 1
  • Khalani “Okonzekera Ntchito Iliyonse Yabwino”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani “Okonzekera Ntchito Iliyonse Yabwino”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukonzekera
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Mmene Mungakonzekerere Kugawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Maulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzikonzekera Mawu Oyamba
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 5/08 tsamba 1

Khalani “Okonzekera Ntchito Iliyonse Yabwino”

1 Yesu atayamba ulendo wina wokalalikira, anakonzekeretsa ophunzira ake. (Mat. 10:5-14) N’zoona kuti tonsefe timatanganidwa, koma kupatula ngakhale mphindi zochepa kuti tikonzekere ulaliki wa khomo ndi khomo, kungatithandizenso ifeyo kukolola zinthu zabwino.—2 Akor. 9:6.

2 Kukonzekera Kwake: Njira yabwino yoyambira kukonzekera ndiyo kuwerenga mabuku amene tikufuna kukagawira kuti tidziwe mfundo zake. Tiyeneranso kuganizira za anthu a m’gawo lathu. Kodi ndi zinthu zotani zimene zimawadetsa nkhawa? Kodi anthu ambiri m’gawo lathu amakhulupirira chiyani? Tingaone zitsanzo za ulaliki mu Utumiki Wathu wa Ufumu ndi m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba kuti tipeze zokanena.

3 China chimene chingatithandize ndicho kumvetsera mosamalitsa pamene zitsanzo zikuchitidwa pa Msonkhano wa Utumiki. M’kupita kwa nthawi tidzazolowera ulaliki wathu, ndipo sitidzafuna nthawi yambiri yokonzekera. Koma ngati nthawi iliyonse imene tikulowa mu utumiki timaganizira zimene tikanene ndi kukonza ulalikiwo mwina ndi mwina, tidzakhala alaliki ogwira mtima kwambiri. Tiyeneranso kutsimikizira kuti chola, kapena kuti chikwama chathu cha m’munda, chili ndi mabuku onse ofunikira.

4 Kodi tingatani kuti tisaiwale ulaliki umene takonzekera? Njira imodzi yothandiza ndiyo kuyeseza ulalikiwo mokweza mawu. Ena amakonda kuyeseza ulaliki wawo pa phunziro labanja. Ena amaona kuti ndi zothandiza kulemba ulaliki wachidule pakapepala, ndipo amayang’ana pa kapepalako akamayandikira pa khomo.

5 Ubwino Wokonzekera: Tikamakonzekera bwino, ulaliki wathu umakhala wogwira mtima kwambiri ndipo chimwemwe chathu muutumiki chimawonjezereka. Kumatithandiza kuti maganizo athu akhazikike ndipo mantha amachepa. Timaganizira kwambiri za mwininyumbayo m’malo movutika ndi kuganiza kuti tinena chiyani. Ndiponso, kudziwa bwino mfundo zimene zili m’mabuku amene tikukagawira kumatithandiza kulankhula motsimikiza pogawira.

6 Malemba amatilimbikitsa kukhala “okonzekera ntchito iliyonse yabwino.” (Tito 3:1) Ndipotu palibe ntchito ina yofunika kwambiri kuposa yolalikira uthenga wabwino. Tikamakonzekera bwino ulaliki wathu, ndiye kuti timalemekeza mwininyumba amene amatimvetsera, komanso Yehova, Mulungu amene timamuimira.—Yes. 43:10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena