Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira February 13
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8, kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, kusonyeza chitsanzo cha mmene tingachitire pogawira Nsanja ya Olonda ya February 15 ndi Galamukani! ya February. Chitsanzo chimodzi chisonyeze ulaliki ukuchitikira pa malo a anthu ambiri.
Mph. 10: Kodi Mukuyendera Limodzi ndi Gulu la Yehova? Nkhani yokambidwa kuchokera mu buku lakuti Gulu Lochita Chifuno cha Yehova, masamba 7 mpaka 10.
Mph. 25: “Uzani Ena za ‘Kuunika kwa Dziko Lapansi.’”a Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Lengezani mayina a abale ndi alongo amene alembetsa upainiya wothandiza. Tchulani nthawi ndi malo amene akonzedwa mwapadera kuti anthu azikumana polowa mu utumiki wa kumunda. Fotokozaninso zitsanzo zosonyeza ndandanda yochitira upainiya wothandiza za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa February 2005 pa tsamba 5.
Nyimbo Na. 224 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 20
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno.
Mph. 15: “Konzani Mipata Yolalikira.”b Pemphani ofalitsa amene amapanikizika ndi mavuto osiyanasiyana kuti afotokoze mmene amakonzera mipata yolalikira.
Mph. 20: “Thandizo Lopezekeratu.”c Ikambidwe ndi mkulu. Kambani mwachidule ndemanga za m’Mabokosi a Mafunso a mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 1998 ndi November 2000.
Nyimbo Na. 1 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira February 27
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pasitetimenti. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa February. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, kusonyeza chitsanzo cha mmene tingachitire pogawira Nsanja ya Olonda ya March 1 kapena Galamukani! ya March.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 25: Mmene Mungagawire buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Tidzagawira buku latsopanoli m’mwezi wa March. Pogwiritsa ntchito mfundo za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2006, masamba 3 mpaka 6, fotokozani ndi kuchitira chitsanzo maulaliki angapo oyenererana bwino ndi gawo lanu. Pemphani omvera kuti afotokoze zokumana nazo zogwira mtima zimene asangalala nazo pogwiritsa ntchito buku latsopanoli, makamaka maphunziro a Baibulo amene ayambitsa.
Nyimbo Na. 148 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 6
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Popeza kuti mathirakiti samavuta kunyamula komanso amakhala okongola, amathandiza poyambitsa makambirano pamene tili mu utumiki wa nyumba ndi nyumba, kumalo a anthu ambiri, ndi pamenenso tikulalikira mwamwayi. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungayambire makambirano pogwiritsa ntchito thirakiti latsopano lakuti Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa. Fotokozani lemba limodzi limene aligwira mawu pa tsamba 2 la thirakitilo.
Mph. 15: “Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukonzekera.”d Chitani chitsanzo chosonyeza ofalitsa awiri akukonzekera kukagawira buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ndiyeno sankhani ulaliki kuchokera mu mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2006 ndipo kambiranani mmene angalalikirire m’mawu awoawo komanso moyenererana ndi anthu a m’gawo lawo. Chitsanzocho chithe pa nthawi imene ofalitsawo akufuna kuyamba kuchitira chitsanzo mokweza mawu zimene amakambiranazo.
Mph. 20: “Pulogalamu Yatsopano ya Msonkhano Wadera.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Tchulani tsiku la msonkhano wadera wotsatira ngati likudziwika. Amene akufuna kubatizidwa ayenera kudziwitsa woyang’anira wotsogolera pasadakhale. Bwereranimo m’nkhani ya patsamba 4 ya m’utumiki wa Ufumu wa August 2004, ya mutu wakuti: “Njira Yatsopano Yobwerezera Zophunziridwa pa Misonkhano Yadera.”
Nyimbo Na. 68 ndi pemphero lomaliza.
[Mawu a M’munsi]
a Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.