Nyimbo 20
Imbani Nyimbo ya Chisangalalo Chaufumu
1. Idzani, tiimbe nyimbo
Yaufumu m’dziko.
Imbitsitsani nyimboyo;
M’dziŵitse Ufumu.
Mapazi ovala mbiri
Akongola ndithu!
Nenani m’mitundu kuti,
‘Chilanditso ncha Ya.’
2. M’nyimbo yathu Yaufumu,
Titama Yehova.
Timamlambira mwamantha
Ndi kumudalitsa.
Mafano olambiridwa
Samapindulitsa.
Koma sitidzachoka kwa
M’lungu wa cho’nadi.
3. M’loŵe m’nyimbo Yaufumu:
“Yehova ndi Mfumu.”
Alamulira mwa Yesu;
Miyamba ikondwa.
Yehova adzaweruza
Dziko m’chilungamo,
Okhulupirika onse
Adzawadalitsa.