Nyimbo 181
Gwirizanani Nawo m’Nyimbo Yaufumu!
1. Pali nyimbo, nyimbo yachilakiko;
Itamanda Wam’mwambamwambayo.
Mawuwo apatsa chiyembekezo.
Imba nafe; Sangalalanitu:
‘Ya ndi Mfumu; Kondwerani.
Miyambanu, Fuulani,’
Nyimbo iyi; Idziŵitsa za Kristu
Onse atamande ufumuwo.
2. Ndi nyimboyi tilengeza Ufumu.
Yesu Kristu; alamula dziko.
Monenedweratu mtundu wabadwa,
Mwana wa Yehova alamula.
‘Mgwadireni Pampandowo.
Ndi Mfumudi. Tidziŵitse!
Phunzirani nyimbo ya Ufumuyi;
Gwadirani Ya ndi kufupidwa.’
3. Nyimboyi odzichepetsa adziŵa.
Njosavuta, njosangalatsadi.
M’dziko lonse khamu laiphunzira,
Nawonso amaitana ena:
‘Lambirani. Mtamandeni,
Adzautsa Akufawo.’
Imbani nafe zitamando za Ya.
Nyimboyi iri yosangalatsa.