Nyimbo 190
Nyimbo kwa Yehova
1. Nyimboyi tiimba lero
Kwa M’lungu wotitsogoza.
Timuyamikira iye
Timtama ndi nyimbo.
Ndiwamkulu muchifundo.
Choncho timuyandikira.
Cho’nadi chatimasula.
Ife tiri ake.
2. Tiyamikira kuŵala,
Kutitsogoza mumdima.
Kuunikira bwinodi
Kumatitonthoza!
Tiyamikira Ufumu;
Sitiyendanso mumdima.
Tilaka zitsenderezo.
Mitima iimba.
3. Tiimba nyimbo mokoma
Ndi kulambira Mulungu
Mwa Kristu tidziŵikitsa
Mapemphero athu:
‘Yehova mwachikondidi,
Landirani zithokozo.
Imvani kupempha kwathu,
Potisamalira.’