Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/02 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 1/02 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu January: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. February: Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. March: Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Tidzayesetse kuyambitsa maphunziro a Baibulo a panyumba. April: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati mwapeza munthu wachidwi paulendo wobwereza, muikeni pa mndandanda wa anthu amene muzigaŵira magazini. Gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji ndi cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo.

◼ Ofalitsa onse obatizidwa amene adzapezeka pa Msonkhano wa Utumiki mlungu wa January 14 adzalandira khadi la Chidziŵitso kwa Madokotala/Chowamasula ku Mlandu ndi makadi a ana awo.

◼ Kuyambira February komanso osapyola March 3, nkhani ya onse imene oyang’anira madera azikamba idzakhala yakuti “Kupeza Chitetezo m’Dziko Loopsa.”

◼ Mipingo iyenera kupanga makonzedwe abwino odzachita Chikumbutso chaka chino Lachinayi, pa March 28, dzuŵa litaloŵa. Ngakhale kuti nkhani ingayambe mofulumira, musayendetse zizindikiro za Chikumbutso kufikira dzuŵa litaloŵa. Funsani odziŵa zanyengo kwanuko kuti mudziŵe nthaŵi yoloŵera dzuŵa m’dera lanulo. Ngakhale kuti n’kwabwino kuti mpingo uliwonse uchite Chikumbutso pawokha, nthaŵi zina si zitheka. Kumene mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi, mpingo umodzi kapena yoposerapo ingapeze malo ena odzagwiritsa ntchito madzulo a tsikuli. Tikupereka malingaliro akuti, ngati kungatheke mapulogalamu akatha pazipita mphindi zosachepera 40 ena asanayambe, kuti onse apindule mokwanira ndi nthaŵiyo, kulonjera alendo ndiponso kulimbikitsa atsopano. Bungwe la akulu liyenera kupanga makonzedwe okomera mpingowo.

◼ Ofufuza nkhani komanso ena afikira abale ambiri kuwapempha chidziŵitso chokhudza Mboni za Yehova ndi gulu lathu. Apempha kuti abalewo alembe mafomu ofufuzira, ayankhe mafunso okhudza zikhulupiriro zathu ndi ziphunzitso. Anthu ngati ameneŵa akafika kwa wofalitsa pampingo, iye aziuza wofunsayo kuti apite ku ofesi ya nthambi ku Lilongwe m’malo moyankha iye mwini.

◼ Woyang’anira wotsogolera akalandira Sitetimenti mwezi uliwonse, azionetsetsa kuti makalata onse oyamikira zopereka za Thumba la Sosaite la Nyumba za Ufumu ndi za ntchito ya padziko lonse zikuŵerengedwa ku mpingo popereka lipoti lotsatira la maakaunti.

◼ Zikuoneka kuti mipingo ina ikuitanitsa magazini ambiri kusiyana ndi amene imagaŵira mwezi uliwonse. Tikukumbutsa onse kuti afunika kuchita khama kulemba palipoti magazini onse amene agaŵira kwa anthu osabatizidwa. Komanso m’pofunika kuyesetsa kugwiritsa ntchito bwino magazini amene timalandira ndipo tingatero mwa kuwagaŵira mu utumiki wa khomo ndi khomo, umboni wa mumsewu, umboni wamwamwayi, pamaulendo obwereza ndi kwa maphunziro a Baibulo. Komabe ngati mwaona kuti mukulandirabe magazini ambiri pambuyo poiona bwino nkhaniyi, tumizani fomu ya M-202 ku nthambi kuti muchepetse chiŵerengero cha oda ya magazini anu. Kutsatira kwanu zimenezi kudzathandiza kuti magazini athu amtengo wapatali asamawonongeke.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena