Kukumbutsa Zopereka Malipoti
Tikupempha kuti malipoti a mpingo azitumizidwa ku Sosaite mwezi uliwonse lisanafike tsiku lachisanu ndi chimodzi la mwezi wotsatira. Taona kuti ilipo mipingo ina imene situmiza malipoti awo miyezi iŵiri, itatu, inayi ngakhale isanu. Kumbukirani kuti tonsefe tili ndi udindo wopereka Malipoti a Utumiki Wakumunda (S-4) panthaŵi yake. Ndipo akulu ndi udindo wawo kuonetsetsa kuti lipoti la mpingo likutumizidwa ku ofesi ya nthambi panthaŵi yake kuti akalisamalire. Komabe, asanatumize Lipoti la Mpingo (S-1), a Komiti ya Utumiki ya Mpingo afunika kuonetsetsa kuti ziŵerengero zonse n’zolondola kuti lipotilo lisakabwezedwe.
Zikukhala ngati mipingo ina ikulemba mathirakiti amene amagaŵira mu utumiki monga timabuku kapena mabulosha pa lipoti. Tikukukumbutsani kuti simuyenera kuŵerengera mathirakiti amene mwagaŵira ndi kuwalemba pa Lipoti la Utumiki Wakumunda kapena pa Lipoti la Mpingo lotumiza ku ofesi ya nthambi. Sitilemba lipoti la mathirakiti amene timagaŵira.
Nanga malipoti ochedwa a wofalitsa kapena mpainiya tiyenera kuwaŵerengera motani? Mwachitsanzo, ngati wofalitsa kapena mpainiya wapereka lipoti lake la September mu October, aperekenso lipoti lake la October. Ndiye malipoti aŵiriwo aŵerengedwe ngati ofalitsa kapena apainiya aŵiri pa S-1 chifukwa wapereka malipoti a miyezi iŵiri.