Gaŵirani Buku la Chimwemwe cha Banja kwa Anthu a Misinkhu Yonse
1 Mnyamata wazaka 11 wa ku California anayamikira buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Iye analemba kuti: ‘Ndikuliyamikira, ndipo ndikulimbikitsa mabanja ena kuti aliŵerenge chifukwa ndi labwino. Likuthandiza banja lathu kukhala mwamtendere ndi mwachimwemwe.’ Zimene zinachitikira mnyamata ameneyu ziyenera kutilimbikitsa kugaŵira buku la Chimwemwe cha Banja kwa anthu a misinkhu yonse. Naŵa malingaliro ena amene mungafune kuyesapo mu utumiki wanu mu February.
2 Mutakumana ndi wachinyamata, munganene kuti:
◼ “Achinyamata ambiri onga iweyo akulingalira zokwatira. Koma kodi chidziŵitso chodalirika pankhani imeneyi tingachipeze kuti? [Yembekezani yankho.] Kaŵirikaŵiri achinyamata amati sakudziŵa ngati ali okonzekera kuloŵa m’banja. Nditakufotokozerako zimene buku ili limanena pankhani imeneyi.” Tsegulani patsamba 14 m’buku la Chimwemwe cha Banja ndi kuŵerenga ndime 3. Ndiyeno m’sonyezeni timitu tonse m’chaputala chimenecho. M’gaŵireni bukulo pachopereka chanthaŵi zonse, ndi kupangana kuti mudzafikenso.
3 Ngati mukulankhula ndi kholo munganene kuti:
◼ “Tikukambirana ndi makolo za malangizo ena othandiza polera ana. Zimenezi zalembedwa m’buku ili lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.” Tsegulani patsamba 55. Ŵerengani ndime 10, kenako Deuteronomo 6:6, 7, mu ndime 11. Ndiyeno m’sonyezeni ziganizo zimene zili ndi mawu opendeketsa m’ndime 12 kufika 16. Pitirizani mwakunena kuti: “Bukuli lathandiza anthu ochuluka kulera ana awo bwino. Ngati mukufuna kuliŵerenga, ndili wosangalala kukupatsani kope ili pachopereka cha K12.00.”
4 Polankhula ndi munthu wachikulire munganene kuti:
◼ “Nditaŵerenga ndemanga yachidule iyi, mundiuze zimene mumaganiza.” Ŵerengani ziganizo ziŵiri zoyambirira za ndime 17 patsamba 169 la buku la Chimwemwe cha Banja. Ndiye m’funseni kuti alankhulepo. Kuchokera pa zimene wanena, mungaŵerenge ndime zina m’bukumo musanaligaŵire pachopereka chanthaŵi zonse.
5 Pobwerera kumene munagaŵira mabuku a Chimwemwe cha Banja, khalani ndi cholinga choyesa kuyambitsa phunziro la Baibulo. Phunziro 8 mu bolosha la Mulungu Amafunanji kapena mutu 15 m’buku la Chidziŵitso angakhale malo abwino oyambira. Padakali pano, tiyeni tiyesetse kuthandiza anthu a misinkhu yonse kuti akhale ndi moyo wabanja wachikristu wachimwemwe.