Misonkhano Yautumiki ya December
Mlungu Woyambira December 2
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.
Mph. 15: “Kodi Ndani Adzamvetsera Uthenga Wathu?” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo mfundo za mu Galamukani! wachingelezi wa March 22, 1987, tsamba 5, zofotokoza chifukwa chake uthenga wathu uli wokopa.
Mph. 20: “Mawu a Mulungu Amapereka Chitsogozo.” (Ndime 1-6) Ndime 1-2 zikhale mawu oyamba a nkhaniyi. (Phatikizanipo buku la Kukambitsirana, masamba 52-4, mukumatchula mwachidule “Zifukwa zophunzirira Baibulo” zinayi.) Khalani ndi ofalitsa okhoza kuti achite zitsanzo za maulaliki osonyezedwa m’ndime 3-6. Pemphani omvetsera kulankhulapo pa (1) mmene mafunso ofunsidwa athandizira kudzutsa chidwi, (2) mmene malemba ogwiritsiridwa ntchito akugwirizanirana ndi nkhani yokambitsirana, (3) mmene ulendo wobwereza wapitirizira ulendo woyamba moyenerera, ndi (4) mmene pempho la phunziro laperekedwera.
Nyimbo Na. 75 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 9
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: Kuthandiza Okalamba Kukhala ndi Phande mu Utumiki. Okalamba okhulupirika ambiri amafunitsitsa kugaŵanamo mu ulaliki pamodzi ndi mpingo, koma ali ndi mavuto akuthupi obwera ndi ukalamba ndi matenda. Pali njira zimene tingawasamalirire moti nkuwaphatikiza pa gulu la utumiki: Dziperekeni kuti mudzawapatsa zoyendera; akonzereni kugwira ntchito m’nyumba zosakhala ndi makwerero ambiri; ikani galimoto pafupi kotero kuti angapumule pamene atopa; dziperekeni kupita nawo pamaulendo awo obwereza; auzeni kuti mungawapereke kunyumba ngati aona kuti sangapitirize. Okalamba amayamikira thandizo loperekedwa kwa iwo. Tchulani njira zina zimene mumasonyezera chisamaliro chotero kwa okalamba kumaloko. Pendani mfundo zazikulu m’nkhani yakuti “Tikuwayamikira Okalambawo!” yopezeka mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 1986, masamba 28-9.
Mph. 20: “Mawu a Mulungu Amapereka Chitsogozo.” (Ndime 7-9) Lankhulani pa “Kufunika kwa Chitsogozo” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 1993, tsamba 3. Fotokozani chifukwa chake maulaliki athu ayenera kugogomezera kufunika kwa kufunafuna thandizo ku magwero apamwamba kwambiri—Mulungu. Khalani ndi wofalitsa kuti achite chitsanzo cha maulaliki a m’ndime 7-8. Gogomezerani kuti chonulirapo chathu chiyenera kukhala cha kuyambitsa phunziro la Baibulo m’buku la Chidziŵitso m’kupita kwa nthaŵi.
Nyimbo Na. 197 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 16
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Perekani malingaliro a mmene tingayankhire malonje a maholide mochenjera. Longosolani makonzedwe apadera a utumiki wakumunda a pa December 25.
Mph. 15: “Kudzipereka Ife Eni Mofunitsitsa.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo ndemanga za mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1984, tsamba 22.
Mph. 20: “Kukondwera Ndi Chiwonjezeko Chimene Mulungu Akupereka.” Nkhani yogwira mtima ya mkulu. Tchulani zochitika kapena umboni wa kuwonjezereka m’maiko otchulidwawo, monga momwe zilili m’ma Yearbook aposachedwa.
Nyimbo Na. 41 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 23
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Tchulani mfundo zina zokambitsirana za m’magazini atsopano zimene zingagwiritsiridwe ntchito mu utumiki mlungu uno. Longosolani makonzedwe apadera a utumiki wakumunda a pa January 1.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo. Kapena mkulu apereke nkhani yakuti “Kupuma Pantchito—Khomo Lotseguka la Ntchito Yateokrase?” ya mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 1996, masamba 24-5.—Onani Insight, Voliyumu 2, tsamba 794, ndime 2-3.
Mph. 20: “Kulembetsa m’Sukulu ya Utumiki Wateokratiki.” Nkhani ya woyang’anira sukulu. Perekani ziŵerengero zakumaloko za olembetsa, ndipo limbikitsani onse amene angalembetse kuti achite motero. Pendani malangizo a nkhani za ophunzira zoperekedwa mu “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokratiki ya 1997.” Limbikitsani onse kukhala ndi makope a Bukhu Lolangiza la Sukulu.
Nyimbo Na. 166 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 30
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Ngati mpingo wanu udzasintha nthaŵi za misonkhano m’chaka chatsopano, perekani chilimbikitso chokoma mtima cholimbikitsa onse kupanga masinthidwe ofunikira ndi kupitirizabe kusonkhana ndi mpingowo mokhazikika panthaŵi zake zatsopano.
Mph. 20: “Thandizo Panthaŵi Yake.” Mafunso ndi mayankho. Sonyezani mfundo zofunika za m’zofalitsa zatsopano zonse ziŵiri.
Mph. 15: Pendani Mabuku Ogaŵira mu January. Tchulani mabuku amene mpingo uli nawo m’stoko. Sankhani aŵiri kapena atatu amene angakhale bwino kuwagwiritsira ntchito m’gawo lanu. Mwa kugwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana, masamba 9-14, pendani mwachidule mawu oyamba oyenerera buku lililonse. Chitani chitsanzo cha ulaliki umodzi kapena maulaliki aŵiri.
Nyimbo Na. 137 ndi pemphero lomaliza.