Nyimbo 100
Tamani Yehova Mulungu Wathu!
1. Tamani! Yehova M’lungu!
Dziŵitsanitu! Ukulu!
Fu’lani! Nyimbo yokondwa!
Dziko ndi kumwamba ndizake.
Zinthu zonse anazipanga.
Zisonyeza mphamvu yake.
Nzeru chilungamo nzambiri;
Ziri zogwirizanadi!
Tamani! Yehova M’lungu!
Dziŵitsanitu! Ukulu!
2. Tamani! Yehova M’lungu!
Dziŵitsanitu! Ubwino!
Fu’lani! Ngwokoma mtima!
Wona ni kukoma mtimako.
Wochititsa mantha munkhondo,
Kwa ofatsa ngwabwinodi.
Ateteza omufunawo.
Apeza kukoma mtima.
Tamani! Yehova M’lungu!
Dziŵitsanitu! Ubwino!
3. Tamani! Yehova M’lungu!
Dziŵitsanitu! Ufumu!
Mveketsa! Ukulu wa Ya
Kungodya zonse zadzikoli!
Nthaŵi yadza! Kristu ndi Mfumu.
Tiyamiketu Yehova.
Tiimbe nyimbo yolakika,
Tisonyeze chidaliro.
Tamani! Yehova M’lungu!
Dziŵitsanitu! Ufumu!