Kupuma Pantchito—Khomo Lotseguka la Ntchito Yateokrase?
KUPUMA pantchito—kwa ambiri ndiko kutha kwa nthaŵi yaitali ya kupsinjika maganizo ndi kuvutika. Pambuyo pokhala omangika ndi ntchito yotopetsa kapena yovuta kwambiri, ambiri amayembekezera kupuma pantchito kumene kudzawatsegulira khomo la zaka zakupuma ndi za ufulu waumwini. Komabe, nthaŵi zambiri khomo limenelo limatsogolera ku kusukidwa ndi kuchita mphwayi. Kusanguluka ndi kuchita zinthu zapamtima sizimapereka chikhutiro chenicheni chimene ntchito imapereka.
Kwa Mboni za Yehova, kupuma pantchito kungatsegule “khomo lalikulu [lomka kukagwira ntchito, NW].” (1 Akorinto 16:9) Ngakhale kuti ukalamba umakhala ndi zovuta ndi ziletso zake, achikulire ena aona kuti angawonjezere utumiki wawo kwa Yehova mwa thandizo lake. Talingalirani za zokumana nazo za Akristu ena achikulire ku Neatherlands. M’chaka chautumiki cha 1995, 269 mwa apainiya (alengezi anthaŵi zonse a Ufumu) oposa 1,223 anali ndi zaka 50 kapena kuposapo. Mwa ameneŵa, 81 anali ndi zaka zakubadwa 65 kapena kuposapo.
Ena amatha kuchita upainiya mwa kungopitiriza kukhala ndi zochita zambiri monga ankachitira pamene anali kugwira ntchito. (Yerekezerani ndi Afilipi 3:16.) Mkristu wina amene akupuma pantchito wadzina lakuti Karel akukumbukira kuti: “Pamene ndinkagwira ntchito yanga yolembedwa, ndinkayamba ntchito ndi 7:30 a.m. Pamene ndinayamba kulandira ndalama zanga zapenshoni, ndinasankha kupitiriza ndi kachitidweko. Ndinkayamba tsiku mwa kuchita umboni wa m’khwalala wa magazini kutsogolo kwa siteshoni ya sitima mmaŵa uliwonse pa 7 koloko.”
Kulinganiza mosamala kulinso mfungulo ya chipambano. (Miyambo 21:5) Mwachitsanzo, ena atha kupatula ndalama zokwanira kuti adzichirikize mu utumiki wawo. Ena asankha kuchepetsa zofuna zaumwini ndi kuloŵa ntchito ya maola ochepa. Taganizirani za Theodore ndi Ann. Iwo anayamba moyo wawo wamuukwati monga apainiya mpaka pamene mathayo abanja anafuna kuti asiye upainiya. Koma mzimu wawo waupaniya unakhalabe wamoyo! Pamene ana awo aakazi ankakula, nthaŵi zonse ankalimbikitsidwa kuchita upainiya. Chofunika koposa ndicho chakuti Theodore ndi Ann anaika chitsanzo chabwino, kaŵirikaŵiri akumatumikira monga apainiya othandiza. Pamene atsikanawo anakulirako, Theodore ndi Ann anayamba kuchepetsa ntchito yolembedwa kuti azikhala ndi nthaŵi yaikulu ya utumiki wakumunda.
Ana awo aakaziwo ataloŵa utumiki wanthaŵi zonse ndi kuchoka panyumba, Ann anayamba upainiya. Tsiku lina analimbikitsa Theodore kusiya ntchito yake. “Tonse aŵirife tingathe kuchita upainiya,” anatero. Theodore anadziŵitsa womlemba ntchito wake za malingaliro ake. Chodabwitsa chinali chakuti mkulu wake wa ntchito anati adzamthandiza mwa kumpatsa ntchito ya maola ochepa, akumati: “Ndiyesa ukufuna kugwirira ntchito yanthaŵi zonse mkulu wako wa ntchito wakumwambaku.” Theodore ndi Ann tsopano akusangalala kuchitira limodzi upainiya.
Ena anayamba upainiya chifukwa cha zochitika m’moyo wawo. Imfa yomvetsa chisoni ya mwana wawo wamkazi ndi mdzukulu wawo wamkazi inachititsa aŵiri okwatirana achikulire kulingalirapo mwakuya za mmene anali kugwiritsirira ntchito zaka zawo zotsala. (Mlaliki 7:2) M’malo mwa kulefulidwa ndi chisoni, iwo anayamba utumiki wanthaŵi zonse, umene tsopano auchita kwa zaka zisanu ndi zitatu!
Zoonadi, pamafunikadi kutsimikiza mtima kwenikweni kuti mukhale mu utumiki wanthaŵi zonse. Mwachitsanzo, Ernst ndi mkazi wake Riek, anayamba upainiya ana awo atangochoka panyumba. Posapita nthaŵi amene kale anali wamalonda mnzake anapatsa Ernst ntchito yaphindu. Ernst anayankha kuti: “Tili ndi wotilemba ntchito wabwino kuposa onse, ndipo sitikufuna kusiya kumtumikira!” Chifukwa chakuti Ernst ndi mkazi wake anakhalabe “olembedwa ntchito” ndi Yehova, mwaŵi wina wa utumiki unawatsegukira. Anatumikira m’ntchito ya dera kwa zaka zoposa 20 ndipo akupitirizabe monga apainiya kufikira lero. Kodi iwo amamva chisoni chifukwa cha njira yawo ya kudzimana? Kale kumbuyoku iwo analemba kuti: ‘Ngati Yehova alola, tikuyembekezera kuchita phwando la zaka zathu 50 za ukwati, limene kaŵirikaŵiri limatchedwa golden anniversary. Koma motsimikiziradi tikuti zaka zathu zabwino koposa zinayamba pamene tinayamba upainiya.’
Ambiri amapeza kuti khomo lotsogolera ku ntchito zowonjezereka limatsogoleranso ku chimwemwe chowonjezereka! Mbale wina amene anayamba upainiya milungu iŵiri pambuyo pa kufikira usinkhu wa zaka 65 akuti: “Ndikunena kuti m’moyo wanga sindinakhalepo ndi nthaŵi yodzala ndi madalitso motere monga zaka khumi zapitazi zaupainiya.” Aŵiri okwatirana amene achita upainiya zaka zoposa zisanu ndi ziŵiri akuti: “Kodi nchiyaninso chimene okwatirana a msinkhu wathu ndipo okhala ndi mikhalidwe yonga yathu ayenera kumachita? Nthaŵi zambiri timaona anthu ofanana nafe m’gawo—atakhazikika bwino panyumba, akumangonenepa, kukalamba, ndi kukonga. Utumikiwu umatichititsa kukhala athanzi m’maganizo ndi kuthupi. Nthaŵi zonse timakhala tonse. Timaseka kwambiri ndi kusangalala nawo moyo.”
Inde, si achikulire onse amene ali ndi mikhalidwe imene imawalola kuchita upainiya. Akristu ameneŵa ayenera kudziŵa kuti Yehova amayamikira zilizonse zimene amatha kuchita mu utumiki wake. (Yerekezerani ndi Marko 12:41-44.) Mwachitsanzo, mlongo wina wopuwala amakhala m’nyumba ya opuwala ndi odwala. Komabe, khomo la ntchito lidakali lotseguka kwa iye! Dokotala wina anamfunsa mmene amagwiritsira ntchito nthaŵi yake yonseyo. Iye akusimba kuti: “Ndinamuuza kuti nthaŵi zonse nthaŵi imandithera. Sanazimvetse zimenezi. Ndinamuuza kuti zimenezi zili choncho chifukwa chakuti masiku anga ngodzala ndi ntchito zokhutiritsa. Sindili wosungulumwa, koma ndimafunafuna ena amene ali osungulumwa ndi kuyesa kuwauza zimene Mulungu wasungira anthu.” Iye akumaliza mwa kunena kuti: “Munthu sangayembekezere zambiri kwa munthu amene ali ndi zaka pafupifupi 80. Ndipempherereni kotero kuti nditsogolerebe ambiri kwa Yehova.”
Kodi muli pamsinkhu wopuma pantchito? Khomo la ntchito zochepa lingakhale lokopa kwambiri, koma sindilo khomo la dalitso lauzimu. Lingalirani za mikhalidwe yanu mwa pemphero. Mwinamwake mungaloŵe pakhomo lotsogolera ku ntchito zowonjezereka mu utumiki wa Yehova.
[Zithunzi patsamba 25]
Kupuma pantchito kungatsogolere ku ntchito zowonjezereka mu utumiki