Kodi Nthaŵi Yopuma Pantchito Ingakhale Nthaŵi Yowonjezera Zochita?
1 Anthu ambiri olimbikira ntchito amalakalaka nthaŵi imene adzapuma pantchito kuti asiyane ndi zovuta za kuntchito. Komabe nthaŵi zambiri kupuma pantchito kumachititsa anthu ena kukhala amphwayi, osoŵa chochita, ndiponso kukalamba msanga. Kusowa chochita chosangalatsa kungapangitse munthu kudziona ngati wopanda phindu. Nyuzipepala ya ku Brazil inanena kuti anthu amene anapuma pantchito anadandaula kuti anali ndi mavuto monga ‘kusasangalala, kukwiyakwiya, kusoŵa moyo wabwino, kudziona ngati osafunika ndipo amafika povutika maganizo chifukwa choona kuti moyo wawo ulibe cholinga.’
2 Mosiyana ndi zimenezi, Akristu ambiri amaona nthaŵi imeneyi kukhala mpata wochitira zinthu zauzimu zochuluka. Mbale wina amene anayamba upainiya patangopita milungu iŵiri atakwanitsa zaka 65 anati: “Pamoyo wanga, sindinakhalepo ndi madalitso ngati amene ndapeza zaka khumi zimene ndakhala ndikuchita upainiya.” Banja lina linati: “Zaka zabwino kwambiri pamoyo wathu zinayamba pamene tinayamba upainiya.” Inde, anthu ambiri amaona kuti kupuma pantchito kumawapatsa mpata wabwino kwambiri wowonjezera zimene amachita mu utumiki ndi kupeza madalitso ochuluka a Yehova.
3 Khalani Otanganidwa ndi Obala Zipatso: Anthu ambiri amene pano anapuma pantchito anakula kulibe zipangizo zimene zafala masiku anozi ndipo anaphunzira kugwira ntchito zolimba ali ana. Ngakhale kuti sangakhale ndi mphamvu monga achinyamata, iwo akadali antchito obala zipatso kwambiri. M’gawo la nthambi ina, apainiya 22 mwa apainiya 100 alionse, omwe ndi abale ndi alongo pafupifupi 20,000, ndi a zaka zosachepera 60. Anthu achikulire ameneŵa amathandiza kwambiri pantchito yolalikira. Zimene akumana nazo pamoyo wawo ndi makhalidwe awo angati a Mulungu amathandiza kwambiri mipingo imene ali.—Yak. 3:17, 18.
4 Kutanganidwa ndi utumiki wachikristu kumathandiza munthu kukhala wathanzi ndiponso wa moyo wabwino. Mlongo wina wachikulire wazaka 84 amene anayamba upainiya atapuma pantchito anati: “Kuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri ndi anthu achidwi kwandithandiza kukhala wochangamuka. Ndilibe galimoto, choncho nthaŵi zambiri ndimayenda pansi. Zimenezi zimandipangitsa kukhala wathanzi.” Banja lina lachikulire limene likuchita upainiya linati: “Utumiki umatipangitsa kukhala oganiza bwino ndiponso amphamvu. Nthaŵi zonse timakhala tili limodzi. Timaseka kwabasi ndipo timasangalala ndi moyo.”
5 Kutumikira Kumene Kukufunika Anthu Olalikira Ambiri: Akristu ena amene anapuma pantchito amene ali bwino pankhani ya zachuma asamukira komwe kukufunika anthu olalikira Ufumu ambiri. Ena awonjezera zimene amachita mu utumiki mwa kutumikira m’madera a chinenero cha dziko lina. Monga mtumwi Paulo, ofalitsa achangu ameneŵa ‘amachita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti akakhale woyanjana nawo.’—1 Akor. 9:23.
6 Banja lina linayamba upainiya litalera ana awo aamuna aŵiri. Atachita upainiya kwa zaka zingapo, anayamba kuphunzira Chitchaina. Posachedwapa, banjali lomwe zaka zawo zikuyandikira 80, linasangalala kuona gulu la Chitchaina limene akhala akusonkhana nalo likukhala mpingo. Mabanja ngati ameneŵa ndi dalitso lalikulu kwambiri!
7 Palibe Kupuma pa Utumiki: Ngakhale kuti anthu ambiri nthaŵi ina amadzapuma pantchito yawo, Mkristu aliyense sapuma potumikira Mulungu. Onse ayenera kukhalabe okhulupirika “kufikira kuchimaliziro.” (Mat. 24:13, 14) N’zoona kuti, chifukwa cha ukalamba, ena sangachite zochuluka potumikira Yehova monga anali kuchitira poyamba. Koma zimalimbikitsa zedi kuwaona akuchita ndi mtima wonse zimene angathe. Mawu a Mulungu amawatsimikizira kuti Yehova sadzaiŵala ntchito yawo ndi chikondi chimene anaonetsa pa dzina lake.—Luka 21:1-4; Aheb. 6:10.
8 Ngati mukuyandikira zaka zopuma pantchito, bwanji osapemphera ndi kulingalira momwe mungagwiritsire ntchito mokwanira kusintha kwa zinthu kumeneko? Ndi thandizo la Mulungu, mungaone kuti nthaŵi yopuma pantchito ndi nthaŵi yanu yowonjezera zochita zimene zimalemekeza Yehova ndi kubweretsa madalitso ambiri.—Sal. 148:12, 13.