Nyimbo 93
Malo Abwino a Yehova Olambiliramo
1. Kachisi wanu ngwabwino,
Atumiki aimamo!
Moyo wanga ufunatu,
Kuti ndi kaimbiremo,
Kuti ndikaimbiremo.
2. Yehova podza kwa inu
Kukonzanso mphamvu zathu,
Mutidyetsa ndi cho’nadi,
Titumikire mwamphamvu,
Titumikire mwamphamvu.
3. Tsiku m’mabwalo anutu
Liposa zikwi kwinanso.
Tikhaletu m’nyumba yanu
Koposa ndi oipawo,
Koposa ndi oipawo.
4. Yehova nditchinjirizo
Kwa onse olungamawo.
Samawamana zabwino
Osalakwa m’nkhola lake,
Osalakwa m’khola lake.