Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 5/1 tsamba 3-4
  • Kodi Tifunikira Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tifunikira Baibulo?
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Osuliza ndi Okaikira
  • Kufunika kwa Chitsogozo
  • Kokha Kumene Tingatembenukire
  • Kodi Nkuti Kumene Mungapeze Chitsogozo Chodalirika?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Zimene Zili M’magaziniyi: Baibulo Lingakuthandizeni Kukhala ndi Moyo Wabwino Kwambiri
    Galamukani!—2019
  • Baibulo—Chitsogozo Chogwira Ntchito cha Munthu Wamakono
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Baibulo ndi Inu
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 5/1 tsamba 3-4

Kodi Tifunikira Baibulo?

OXANA, msungwana wa ku Russia, anakondwera pamene anawona Baibulo logulitsidwa ndi wogulitsa mabuku m’khwalala ku Moscow. Bwenzi lake, John, amene anachokera ku dziko kumene Mabaibulo anali kupezeka mosavuta, anachita chidwi ndi chikondwerero cha Oxana. “Ineyo​—wosakhulupirira kukhalako kwa Mulungu​—ndinafuna kumgulira,” iye anavomereza motero. Ngakhale kuti Oxana poyamba anakana, iye pomalizira analandira mphatsoyo kwa John.

Ambiri, mofanana ndi Oxana, ali ndi chikhumbo chachikulu cha kukhala ndi Baibulo. Zimenezi zili choncho makamaka m’maiko mmene ilo lakhala loletsedwa kwa zaka zambiri. Mwachitsanzo, ofalitsa magazini ino akugwira ntchito zolimba kuti akwaniritse kusoŵa kwa Mabaibulo m’maiko amene kale anali Soviet Union, kudzanso m’mbali zina za dziko. Kwa nthaŵi yoyamba, anthu ambiri m’madera ameneŵa akhala ndi mwaŵi wakupenda Baibulo mosamalitsa​—ndipo ambiri akukopeka ndi uthenga wake wamphamvu.

Osuliza ndi Okaikira

Mosiyana ndi zimene zatchulidwa pamwambapa, makamaka kumpoto kwa Ulaya, Baibulo silimaŵerengedwa, koma limangosiidwa pashelufu ya mabuku likukutidwa ndi fumbi. “Ndimbiri yakale!” ena amatero, akumawonjezera kuti, “Linalembedwera nyengo ina. Nlosafunika konse kwa munthu wamakono.” Ngakhale atsogoleri achipembedzo otchuka apereka ndemanga zapoyera zimene zimaluluza Baibulo. Akibishopu wa Anglican Desmond Tutu wasimbidwa mu The Star, nyuzipepala ya ku South Africa, kuti anati: “Pali mbali zina za Baibulo zimene zilibe phindu lokhalitsa.” Ndemanga zonga zimenezi zachititsa ambiri kudabwa kuti ndichikhulupiriro chotani chimene ayenera kukhala nacho m’Baibulo.

Kufunika kwa Chitsogozo

Osuliza ndi okhulupirira omwe ayenera kuvomereza kuti, kuposa ndi kalelonse, dziko lifunikira zothetsera mavuto zogwira ntchito. “Ngati munthu saphunzira msanga kulamulira liŵiro la kusintha kwa zochita zake limodzi ndi za anthu onse,” analemba motero Alvin Toffler m’buku lake la Future Shock, “tidzakhala ndi kunyonyotsoka kwakukulu . . . kwa zinthu.” Chenjezo limenelo linaperekedwa zaka zoposa 20 zapitazo. Kunyonyotsoka kwa zinthu kumene Toffler ananena kukuwonekera kukhala kukuchitika tsopano lino.

Pamene zaka za zana lino zikuyandikira mapeto ake, zitukuko za luso lazopangapanga ndi nthanthi za anthu zalephera kudzetsa bata padziko lonse. Ziyembekezo zaposachedwapa za dongosolo la dziko latsopano zachititsa kugwiritsa mwala, ndipo miyoyo ya ambiri yangokhala nkhondo yomenyera kupitiriza kukhalako.

Ziŵerengero zimasonyeza kuti kusiyana m’zachuma pakati pa olemera ndi osauka kwakhala kwakukulu koposa. Kufufuza kwaposachedwapa kukusonyeza kuti 82.7 peresenti ya chuma cha dziko ili m’manja mwa anthu okwanira 20 peresenti chabe. Kodi kungakhalenso kodabwitsa kuti nkhondo, njala, matenda, zipoloŵe, ndi kusaweruzika zili zofala m’maiko ambiri? Chitsenderezo cha kuchita ndi mkhalidwe womanyonyotsoka wa moyo chikuchititsa anthu kupsinjika mtima kwambiri. Chotero, ngakhale mbali yofunika kwambiri ya chitaganya, banja, likunyonyotsoka.

Ngakhale kuti ambiri, mofanana ndi Toffler, akulingalira kuti lili thayo la munthu “kufunafuna njira zatsopano kotheratu zopezera bata ndi chisungiko,” umboni umatsimikizira kuti anthu ngosakhoza kupereka zothetsera mavuto zawozawo.

Kokha Kumene Tingatembenukire

Baibulo Lopatulika, limene linayamba kulembedwa pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, silinasinthe konse m’zaka mazana ambiri. Malamulo ake amkhalidwe ngosasintha. Mwachitsanzo, mawu a Yeremiya 10:23 atsimikizira kukhala owona lerolino kuposa ndi kalelonse: “Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Ngati anthu sakhoza kulongosola njira yawo, ndani angathe? Baibulo limatchula Magwero okha owona a chitsogozo: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.”​—Yesaya 48:17.

Kupyolera m’masamba a Baibulo, Yehova Mulungu amatiphunzitsa kudzithandiza ife eni. Iwo ngodzala ndi uphungu umene umatisonyeza njira imene tiyenera kuyendamo. Uphungu wake ngwofunika lerolino monga momwe unaliri panthaŵi ya kulembedwa kwake. Nkhani yotsatira idzapenda mmene Baibulo liliri logwira ntchito m’nthaŵi yathu yamakono. M’nkhani zosiyanasiyana, kuyambira pa umoyo ndi chuma, moyo wabanja, ndi khalidwe la munthu, mudzakhoza kuwona kuti Baibulo lilidi thanthwe lolimba pakati pa mikhalidwe yamakono yomasinthasintha ya dziko.

[Chithunzi patsamba 4]

Baibulo lili mnangula wa bata m’dziko loŵinduka lamakono

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena