Nyimbo 209
Tsatirani Mfumu Yankhondo!
1. Tiri nayo nyimbo ya kwa Yehova;
Yaulemelero ndi ufumu.
Tiri ndi uthenga wa anthu amve
Ndi ulamuliro wa kunena.
(Korasi)
2. Ankhondo a Mulungu, dzukanitu
Pansi pa Ngwazi ya a ufulu;
Tengani chikopa cha ku uzimu,
Ndi chisoti cha chipulumutso.
(Korasi)
3. Sitingapambane mumphamvu yathu;
Mwa tokha sitingathe nkhondoyo.
Koma mwa Mulungu tinga pambane,
Kudziŵitsa dzina la Yehova.
(KORASI)
Pitani! (Inde!)
Musawope! (Musawope!)
Monga gulu lankhondo
Lomenyana ndi mdani;
Tsatira ni Kristu Mfumu yankhondo.
Mtsatireni, tidzalaka!