Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/96 tsamba 1
  • Kudzipereka Ife Eni Mofunitsitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudzipereka Ife Eni Mofunitsitsa
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Kudzipereka Ife Eni Mwaufulu Kuchita Ntchito Iliyonse Yabwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Njira Zowonjezerera Utumiki Wanu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Kupita Kwanu Patsogolo Kuonekere
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Muzikumbukira Atumiki a Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 12/96 tsamba 1

Kudzipereka Ife Eni Mofunitsitsa

1 Wamasalmo Davide analosera kuti anthu a Yehova “adzadzipereka eni ake mofunitsitsa”; ndiko kuti, monga “antchito odzifunira osazengereza.” (Sal. 110:3, NW, mawu amtsinde) Ndithudi zimenezi zikukwaniritsidwa m’gulu lathu la abale la padziko lonse. M’zaka zautumiki zonse zinayi zapitazi, anthu a Yehova awonongera maola oposa 1,000,000,000 pa kufalitsa uthenga wabwino wa Ufumu. Ndipo pali njira zambiri, kuwonjezera pa kulalikira ndi ntchito yopanga ophunzira, mmene tingadziperekere mofunitsitsa kuti tithandize ena.

2 Mmene Tingasonyezere Kufunitsitsa Kwathu: Ena mumpingo angafune thandizo kuti afike pamisonkhano. Bwanji osadzipereka kuti muzipita nawo? Ena angakhale odwala, athanzi lofooka, kapena angakhale m’chipatala. Kodi mungayambe inu kuwachezera kapena kuwathandiza m’njira ina yake? Pangakhale munthu kapena banja lofunikira chilimbikitso. Kodi mwaganizapo za kuwaitana ameneŵa kuti adzakhalepo pa phunziro lanu la banja nthaŵi zina? Mpainiya kapena wofalitsa wina angafune wopita naye mu utumiki. Bwanji osadzipereka kuti mugwire naye ntchito mu utumiki? Izi ndizo zina za njira zimene tingachitire chokoma kwa awo apabanja lachikhulupiriro.—Agal. 6:10.

3 Abale angasonyeze kuti ali ofunitsitsa kugwiritsiridwa ntchito m’gulu la Yehova mwa kuyesetsa kufitsa ziyeneretso za akulu ndi atumiki otumikira. (1 Tim. 3:2-10, 12, 13; Tito 1:5-9) Pamene chiŵerengero chathu chipitiriza kukula, pamafunikira abale oyeneretsedwa amene ali ofunitsitsa kutsogolera pakulalikira ndi kuphunzitsa ndi pakuŵeta mipingo.—1 Tim. 3:1.

4 Mwinamwake ena a ife tingadzipereke mokulirapo mu utumiki wa Yehova mwa kulembetsa monga apainiya othandiza nthaŵi ndi nthaŵi. Ndiyenonso, mwa kupanga masinthidwe abwino a zinthu zingapo m’ndandanda yathu, tingathe kumachita zimenezo nthaŵi zonse kapena ngakhale kuyamba utumiki wa upainiya wanthaŵi zonse. Kodi mikhalidwe yathu ingatilole kupita kumalo ofunikira thandizo lowonjezereka? Kodi tingadzipereke kukatumikira pa Beteli ndipo chotero tikumathandizira mwachindunji kupita patsogolo kwa ntchito ya padziko lonse? Palinso zambiri zimene zikuchitidwa pakumanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Misonkhano, ndi nthambi kuzungulira dziko lonse, kumene mzimu wofunitsitsa kugwira ntchito ukufunika kwambiri. Awo amene adzipereka pantchito zabwino zimenezi akuyamikiridwa kwambiri, ndipo adalitsidwa kwambiri!—Luka 6:38.

5 Zino ndi nthaŵi zosangalatsa kwambiri. Yehova, mwa mzimu wake, akuchita ntchito yodabwitsa padziko lapansi ndi anthu ake ofunitsitsa! Nthaŵi zonse pamene Yehova, mwa gulu lake, akutipempha kuti tigaŵanemo m’ntchito yowonjezereka ya Ufumu, tichita bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikali kudzipereka mofunitsitsa?’ Ndiyeno mwapemphero tiyenera kusanthula mtima wathu ndi mikhalidwe yathu. Kudzipereka kwathu kwaumulungu kudzatisonkhezera kuchita zonse zomwe tingathe mu utumiki wopatulika, choncho tikumasangalatsa kwambiri mtima wa Yehova!—Zef. 3:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena